Yoweli 1:1-20

1  Yehova analankhula+ kudzera mwa Yoweli mwana wa Petueli kuti:  “Tamverani inu akulu ndipo mutchere khutu inu nonse okhala m’dzikoli.+ Kodi zinthu izi zinachitikapo m’masiku anu, kapena m’masiku a makolo anu?+  Fotokozerani ana anu za zinthu zimenezi. Ana anu adzafotokozere ana awo, ndipo ana a ana anuwo adzafotokozerenso m’badwo wotsatira.+  Zinthu zimene mbozi zinasiya zinadyedwa ndi dzombe.+ Zimene dzombelo linasiya zinadyedwa ndi ana a dzombe oyenda pansi opanda mapiko ndipo zimene ana a dzombe oyenda pansiwo anasiya zinadyedwa ndi mphemvu.+  “Galamukani zidakwa inu.+ Lirani ndipo fuulani+ chifukwa cha vinyo wotsekemera*+ inu nonse okonda kumwa vinyo, pakuti vinyoyo wachotsedwa pakamwa panu.+  Pali mtundu umene walowa m’dziko langa. Mtunduwo ndi wamphamvu ndipo anthu ake ndi osawerengeka.+ Mano ndiponso nsagwadwa zawo zili ngati za mikango.+  Iwo achititsa mtengo wanga wa mpesa kukhala chinthu chodabwitsa+ ndipo mtengo wanga wa mkuyu ausandutsa chitsa.+ Nthambi za mitengo imeneyi azichotsa makungwa n’kuzitayira kutali.+ Mphukira zake azichotsa makungwa ndipo zauma.  Lirani momvetsa chisoni ngati mmene amalirira namwali amene wavala chiguduli*+ polirira mwamuna amene anali kufuna kumukwatira.  “Nsembe yambewu+ ndi nsembe yachakumwa+ zachotsedwa m’nyumba ya Yehova. Ansembe, atumiki+ a Yehova, alira.+ 10  Munda wawonongedwa+ ndipo nthaka ikulira+ pakuti mbewu zawonongedwa. Vinyo watsopano wauma+ ndipo mafuta atha.+ 11  Alimi achita manyazi+ chifukwa cha tirigu ndi barele ndipo osamalira minda ya mpesa akulira mofuula. Zili choncho chifukwa chakuti zokolola za m’munda zawonongeka.+ 12  Kukondwera kwachoka pamaso pa ana a anthu.+ Ndithu mtengo wa mpesa wauma ndiponso mtengo wa mkuyu wafota. Mtengo wa makangaza* komanso mtengo wa kanjedza, mtengo wa maapozi ndi mitengo yonse yakuthengo yauma.+ 13  “Dzimangirireni m’chiuno ndipo dzigugudeni pachifuwa,+ inu ansembe. Lirani mofuula, inu atumiki a paguwa lansembe.+ Lowani, valani ziguduli usiku wonse inu atumiki a Mulungu wanga, pakuti nsembe yambewu+ ndi nsembe yachakumwa zachotsedwa m’nyumba ya Mulungu wanu.+ 14  Konzekerani nthawi yosala kudya.+ Itanitsani msonkhano wapadera.+ Sonkhanitsani pamodzi akulu ndi anthu onse okhala m’dzikoli kuti akumane kunyumba ya Yehova Mulungu wanu+ ndipo alirire Yehova kuti awathandize.+ 15  “Kalanga ine! Tsiku lija likufika.+ Tsiku la Yehova lili pafupi.+ Tsikulo lidzafika ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse. 16  Kodi chakudya sanatichotsere pamaso pathu? Kodi kukondwera ndi kusangalala sizinachotsedwe m’nyumba ya Mulungu wathu?+ 17  Nkhuyu zouma zawonongeka mafosholo ali pamwamba pake. Nkhokwe zawonongedwa. Nyumba zosungiramo zinthu zapasulidwa, pakuti mbewu zatha. 18  Ziweto zausa moyo. Gulu la ng’ombe likuyendayenda mosokonezeka pakuti kulibe msipu woti zidye.+ Ndiponso gulu la nkhosa ndi limene lalangidwa chifukwa cha uchimo. 19  “Ine ndidzaitana inu Yehova,+ pakuti moto wawononga malo odyetserako ziweto m’chipululu ndipo moto walawilawi wanyeketsa mitengo yonse yakuthengo.+ 20  Chifukwa chakuti mitsinje ya madzi yauma,+ ndipo moto wawononga malo odyetserako ziweto m’chipululu, zilombo zakutchire nazonso zikukufunani kwambiri.”+

Mawu a M'munsi

Ena amati “wonzuna.”
Ena amati “saka.”
“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu, mwina chifukwa choti njere zake zimaoneka ngati chimanga.