Aefeso 6:1-24

6  Ananu, muzimvera makolo anu+ mwa+ Ambuye, pakuti kuchita zimenezi n’chilungamo.+  “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako,”+ ndilo lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo:+  “Kuti zinthu zikuyendere bwino, ndiponso kuti ukhale ndi moyo wautali padziko lapansi.”+  Inunso abambo, musamapsetse mtima ana anu,+ koma muwalere+ m’malangizo*+ a Yehova* ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe+ kake.  Akapolo inu, muzimvera anthu amene ndi ambuye anu.+ Muziwaopa ndi kuwalemekeza+ moona mtima, monga mmene mumachitira ndi Khristu.  Osati mwachiphamaso ngati ofuna kukondweretsa anthu,+ koma monga akapolo a Khristu, ochita chifuniro cha Mulungu ndi moyo wonse.+  Khalani akapolo amaganizo abwino, monga otumikira Yehova+ osati anthu,  pakuti mukudziwa kuti chabwino chilichonse chimene wina aliyense angachite adzachilandiranso kwa Yehova,+ kaya munthuyo akhale kapolo kapena mfulu.+  Inu ambuye, muzichitiranso akapolo anu chimodzimodzi ndipo muleke kuwaopseza,+ pakuti mukudziwa kuti Ambuye wa nonsenu, wa iwowo ndi wa inuyo,+ ali kumwamba ndipo alibe tsankho.+ 10  Potsiriza ndikuti, pitirizani kupeza mphamvu+ kuchokera kwa Ambuye ndiponso kuchokera ku mphamvu+ zake zazikulu. 11  Valani zida zonse zankhondo+ zochokera kwa Mulungu kuti musasunthike polimbana ndi zochita zachinyengo+ za Mdyerekezi, 12  chifukwa sitikulimbana+ ndi anthu athupi la magazi ndi nyama ayi, koma ndi maboma,+ maulamuliro,+ olamulira dziko+ a mdimawu, ndi makamu a mizimu yoipa+ m’malo akumwamba. 13  Pa chifukwa chimenechi, nyamulani zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu+ kuti musadzagonje m’tsiku loipa, ndipo mutachita zonse bwinobwino, mudzathe kulimba.+ 14  Chotero khalani olimba, mutamanga kwambiri choonadi+ m’chiuno mwanu,+ mutavalanso chodzitetezera pachifuwa chachilungamo,+ 15  mapazi+ anu mutawaveka nsapato zokonzekera uthenga wabwino wamtendere.+ 16  Koposa zonse, nyamulani chishango chachikulu chachikhulupiriro,+ chimene mudzathe kuzimitsira mivi yonse yoyaka moto+ ya woipayo. 17  Komanso landirani chisoti cholimba+ chachipulumutso, ndiponso lupanga+ la mzimu,+ lomwe ndilo mawu a Mulungu.+ 18  Pamene mukutero, muzipemphera pa chochitika chilichonse mu mzimu,+ mwa mtundu uliwonse wa pemphero+ ndi pembedzero. Kuti muchite zimenezi, khalani maso mosalekeza ndi kupemphera mopembedzera m’malo mwa oyera onse, 19  kuphatikizapo ineyo. Chitani zimenezi kuti ndikatsegula pakamwa panga kuti ndilankhule, ndizitha kulankhula+ mwaufulu+ kuti ndidziwitse ena chinsinsi chopatulika cha uthenga wabwino,+ 20  umene ndili kazembe+ wake womangidwa ndi unyolo, ndiponso kuti ndilankhule za uthengawo molimba mtima monga mmene ndiyenera kuchitira.+ 21  Tsopano, kuti mudziwenso mmene zinthu zikuyendera pa moyo wanga ndi mmene ine ndilili, Tukiko,+ m’bale wokondedwa ndiponso mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye, adzakufotokozerani zonse.+ 22  Ndamutumiza kwa inu ndi cholinga chimenechi, kuti mudziwe mmene zinthu zilili kwa ife ndi kuti atonthoze mitima yanu.+ 23  Mtendere ndi chikondi ndiponso chikhulupiriro zochokera kwa Mulungu Atate, ndi kwa Ambuye Yesu Khristu, zikhale pa abalenu. 24  Kukoma mtima kwakukulu+ kukhale pa onse amene ali ndi chikondi chenicheni pa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.
Onani Zakumapeto 2.