Aefeso 1:1-23

1  Ine Paulo, mtumwi+ wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu,+ ndikulembera oyera amene ali ku Efeso, okhulupirikawo+ okhala mogwirizana+ ndi Khristu Yesu, kuti:  Kukoma mtima kwakukulu,+ ndi mtendere+ wochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi kwa Ambuye Yesu Khristu, zikhale nanu.  Atamandike Mulungu, Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu,+ pakuti watidalitsa+ ndi dalitso lililonse lauzimu m’malo akumwamba+ mogwirizana ndi Khristu.  Wachita zimenezi monga mmene anatisankhira+ kuti tikakhale ogwirizana ndi Yesuyo dziko lisanakhazikitsidwe,+ kuti tikakhale oyera ndi opanda chilema+ pamaso pa Mulungu m’chikondi.+  Pakuti anatisankhiratu+ kuti adzatitenga+ kukhala ana ake+ kudzera mwa Yesu Khristu, malinga ndi zomukomera iyeyo ndiponso chifuniro chake.+  Anatero kuti kukoma mtima kwakukulu kwaulemerero+ kumene anatisonyeza kudzera mwa wokondedwa wake+ kutamandike.+  Kudzera mwa iyeyu, tinamasulidwa ndi dipo* la magazi+ ake, inde, takhululukidwa+ machimo athu, malinga ndi chuma cha kukoma mtima kwake kwakukulu.+  Iye anatipatsa mochuluka kukoma mtima kumeneku mwa nzeru zonse+ ndi kuzindikira konse,  moti anatiululira chinsinsi chopatulika+ cha chifuniro chake. Chinsinsicho n’chogwirizana ndi zokomera mwiniwakeyo ndiponso zimene anafuna mumtima mwake,+ 10  kuti akakhazikitse dongosolo+ lake, ikadzatha nyengo yonse ya nthawi zoikidwiratu.+ Dongosolo limenelo ndilo kusonkhanitsanso+ zinthu zonse pamodzi mwa Khristu,+ zinthu zakumwamba+ ndi zinthu zapadziko lapansi.+ Inde, kuzisonkhanitsanso mwa iye. 11  Mogwirizana ndi iyeyo tinaikidwa kukhala odzalandira cholowa,+ pakuti anatisankhiratu mwa kufuna kwake, iye amene amayendetsa zinthu zonse mogwirizana ndi chifuniro chake.+ 12  Anachita zimenezo kuti ife tichititse kuti ulemerero wake utamandike,+ ifeyo amene takhala oyamba kukhala ndi chiyembekezo mwa Khristu.+ 13  Koma inunso munakhala ndi chiyembekezo mwa iye mutamva mawu a choonadi,+ omwe ndi uthenga wabwino wonena za chipulumutso chanu.+ Kudzeranso mwa iye, mutakhulupirira munaikidwa chidindo+ cha mzimu woyera wolonjezedwawo,+ 14  umene ndi chikole+ cha cholowa chathu cham’tsogolo,+ kuti anthu a Mulungu+ adzamasulidwe ndi dipo,+ n’cholinga choti iye adzatamandidwe ndi kupatsidwa ulemerero. 15  Ndiye chifukwa chake inenso, kuyambira pamene ndinamva za chikhulupiriro chimene muli nacho mwa Ambuye Yesu ndi mmene mumachisonyezera m’zochita zanu ndi oyera onse,+ 16  sindileka kuyamika Mulungu chifukwa cha inu. Ndikupitirizabe kukutchulani m’mapemphero anga,+ 17  kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate waulemerero, akupatseni mzimu wa nzeru+ ndi kuti mumvetse zimene Iye akuulula mogwirizana ndi kumudziwa molondola.+ 18  Popeza maso+ a mtima wanu aunikiridwa,+ ndikukutchulanibe m’mapemphero anga kutinso mudziwe chiyembekezo+ chimene anakuitanirani, chuma chaulemerero+ chimene wasungira oyera monga cholowa,+ 19  ndi kukula kwa mphamvu zake zopambana+ zimene wazipereka kwa ife okhulupirira. Kukula kumeneko n’kogwirizana ndi ntchito+ ya mphamvu yake yodabwitsa, 20  imene waigwiritsa ntchito pa Khristu pamene anamuukitsa kwa akufa+ ndi kumukhazika kudzanja lake lamanja+ m’malo akumwamba.+ 21  Anamuika pamwambamwamba kuposa boma lililonse, ulamuliro uliwonse, amphamvu onse, ambuye onse,+ ndi dzina lililonse loperekedwa kwa wina aliyense,+ osati mu nthawi* ino yokha,+ komanso imene ikubwerayo.+ 22  Mulungu anaikanso zinthu zonse pansi pa mapazi a iyeyo,+ ndipo anamuika mutu wa zinthu zonse+ chifukwa cha mpingo, 23  umene ndi thupi lake.+ Mpingowo ndi wodzaza+ ndi iye, amene amadzaza zinthu zonse mokwanira.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.