Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

JW LIBRARY

Zinthu Zopezeka pa JW Library

Zinthu Zopezeka pa JW Library

Zinthu Zopezeka M’Baibulo

  • Sankhani Baibulo lomwe mukufuna kugwiritsa ntchito pa Mabaibulo 6 omwe alipo.

  • Yerekezani zimene Mabaibulo osiyanasiyana amanena podina nambala ya vesilo.

  • Onani mawu ogwirizana ndi vesilo podina chizindikiro cha mawu a m’musi kapena cha lifalensi.

 

Mmene Mungawerengere

  • Ngati mukugwiritsa ntchito tabuleti kapena chipangizo chilichonse cha m’manja, yendetsani ndi chala chanu kumanzere kapena kumanja kuti mupite patsamba lotsatira.

  • Ikani mabukumaki pa vesi kapena chaputala chimene mukuwerenga kuti musavutike kuchipeza mukafuna kupitiriza kuwerenga.

  • Gwiritsani ntchito gawo losonyeza zimene mwawerenga m’mbuyo kuti mupeze zimene mwawerenga posachedwapa.

  • Gwiritsani ntchito gawo lofufuzira kuti mufufuze mawu m’nkhani imene mukuwerenga.