DECEMBER 31, 2025
ZATSOPANO
Pulogalamu ya JW Library Sign Language® Sizipezekanso
Tasiya kugwiritsa ntchito pulogalamu ya JW Library Sign Language ndipo sizipezekanso pa app store. Tsopano zinthu zonse zimene zinali mupulogalamuyi zizipezeka mu JW Library, imene ili ndi zinthu zina zothandiza pa chinenero chamanja. Zinthu zina ziwonjezeredwa kutsogoloku.

