Pitani ku nkhani yake

MARCH 4, 2019
ZATSOPANO

Kawerengedwe ka Zinenero Kasintha

Kawerengedwe ka Zinenero Kasintha

Njira yowerengera zinenero zomwe mukupezeka mabuku ndi zinthu zina pawebusaiti yathu yasintha. Tsopano chiwerengero cha zinenero zomwe zikuoneka pa kabokosi kakuti “Sankhani Chinenero Chanu” sichikuphatikizapo zinenero zofanana mayina zomwe zimangosiyana kalembedwe kake. Mwachitsanzo, zinenero za Chisebiya (Chisililiki) komanso Chisebiya (Chiromani) tsopano ziziwerengedwa ngati chinenero chimodzi, osati ziwiri. Chifukwa cha zimenezi, nambala ya zinenero yomwe ikuoneka pa kabokosi kakuti “Sankhani Chinenero Chanu” yatsika. M’tsogolomu kusintha kumeneku kuyamba kuonekanso pa LAIBULALE YA PA INTANETI komanso pa JW Library app.