Pitani ku nkhani yake

16 JANUARY, 2017
RUSSIA

Khoti la Apilo M’dziko la Russia Lakana Apilo ya a Mboni

Khoti la Apilo M’dziko la Russia Lakana Apilo ya a Mboni

Mkulu woimira boma pamilandu m’dziko la Russia anaopseza kuti atseka likulu la Mboni za Yehova m’dzikolo. A Mboni za Yehova anapanga apilo za nkhaniyi ponena kuti zimene mkulu woimira boma pa milanduyu ananena ndi zosemphana ndi malamulo. Koma pa 16 January, 2017, Khoti la mu mzinda wa Moscow linakana apiloyo. Oweruza milandu atatu a khotilo sanagwirizane ndi zimene oimira Mboni za Yehova ananena pa nkhaniyi ndipo anapereka chigamulo chawo pambuyo poimitsa mlanduwu kwa 10 minitsi. Chigamulo chimenechi chikugwirizana ndi chimene Khoti la m’chigawo cha Tverskoy linapereka pa 12 October, 2016, chomwe chinali chokomera mkulu woimira boma pa milanduyo. Chenjezo loti atseka likulu la Mboni za Yehova, linaperekedwa pa 2 March, 2016 ndipo tsopano ndi loti likhoza kutsatiridwa. Komabe, sizikudziwika bwinobwino kuti chenjezo limeneli likhoza kukhudza bwanji ufulu wopembedza wa a Mboni m’dziko la Russia.