Pitani ku nkhani yake

OCTOBER 9, 2013
GERMANY

Mwambo Wokhazikitsa Chipilala Chokumbukira wa Mboni za Yehova Amene Anapulumuka Nkhanza ku Germany

Mwambo Wokhazikitsa Chipilala Chokumbukira wa Mboni za Yehova Amene Anapulumuka Nkhanza ku Germany

SELTERS, Germany—Pa June 21, 2013, bwanamkubwa wa tauni ya Selters pamodzi ndi akuluakulu ena a tauniyi, anakhazikitsa chipilala chokumbukira bambo wina, dzina lake Max Liebster, yemwe anamwalira mu 2008. Bamboyu anali wa Mboni za Yehova ndipo m’mbuyomo, anamangidwa ndiponso kuzunzidwa ndi chipani cha Nazi kwa zaka zoposa 5. Mwambowu unachitikira m’dera la Lautertal-Reichenbach m’tauni yomweyi ya Selters. Pamwambo wokhazikitsa chipilalawu panalinso anthu ena a m’derali komanso mkazi wa malemuwo, Mayi Simone Liebster, omwenso ndi a Mboni za Yehova.

Bambo Max Liebster anali a mtundu wachiyuda. Izi zinachititsa kuti m’chaka cha 1939, amangidwe ndi apolisi a Gestapo ndipo anayamba kuzunzidwa m’ndende zosiyanasiyana zoposa 5. Ndendezi zinali Sachsenhausen, Neuengamme, Auschwitz, Buna, ndi Buchenwald. Ndipo abale awo okwana 8 anafera m’ndende zimenezi. Bambo awo a Liebster anali m’gulu la anthu amene anafera kundende zimenezi ndipo a Max Liebster ananyamula okha mtembo wa bambo awo mpaka kumalo amene ankawotcherako mitembo. Nkhanza zonsezi zinkachitika pa nthawi imene Hitler ankalamulira dziko la Germany.

Bambo Liebster ali kundende zozunzirako anthu ankagwirizana kwambiri ndi akaidi a Mboni za Yehova. Moti m’chaka cha 1945 atangotulutsidwa kundende, anabatizidwa kukhala wa Mboni za Yehova. Pachipilala chokumbukira bambowa pali kachitsulo kamene analembapo mawu akuti, “chikhulupiriro cha a Liebster chinawathandiza kupirira pa nthawi imene ankazunzidwa ndipo sitidzaiwala kukhulupirika kwawo.” Iwo anamwalira ali ndi zaka 93, mu 2008.

Papepala loitanira anthu kumwambowu panalembedwa mawu akuti: “Bambo Liebster ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti mfundo zachikhristu zingathandize kwambiri anthu.” Bambo Wolfram Slupina, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova ku Germany, ananena kuti: “Ndife osangalala kuti mmodzi wa anthu olimba mtima achipembedzo chathu akukumbukiridwa chifukwa chosafuna kusiya zimene amakhulupirira ngakhale kuti ankazunzidwa. Chipilalachi chikutitsimikizira mphamvu ya uthenga wa m’Baibulo wolimbikitsa mtendere ndi mgwirizano, umene a Mboni za Yehova amayesetsa kuutsatira.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera m’mayiko ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

German: Wolfram Slupina, tel. +49 6483 41 3110