Georgia
Msonkhano Wapadera Woyamba Kuchitika Mumzinda wa Tbilisi ku Georgia
Msonkhano wapaderawu womwe unali woyamba kuchitika ku Georgia, unali wosangalatsa chifukwa panali chakudya chambiri chauzimu, kuchereza alendo, komanso chionetsero cha chikhalidwe ndi mbiri ya dzikolo.
Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe Lathandiza Kuti a Mboni za Yehova Akhale ndi Ufulu Wopembedza ku Georgia
Chigamulo chaposachedwapa cha Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe chikuteteza ufulu wa a Mboni wosonkhana pamodzi n’cholinga cholambira Mulungu komanso kuuza ena zimene amakhulupirira mwamtendere.
Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya Lagamula Mlandu Motsatira Malamulo ku Georgia
Pa October 7, 2014, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linagamula mokomera a Mboni za Yehova ku Georgia. Akuluakulu a dzikoli anapezeka olakwa chifukwa chophwanya ufulu wachipembedzo wa Mboni za Yehova komanso maufulu awo ena.