Pitani ku nkhani yake

30 JANUARY, 2017
ERITREA

Wa Mboni Winanso Wafa ku Eritrea Atatulutsidwa M’ndende

Wa Mboni Winanso Wafa ku Eritrea Atatulutsidwa M’ndende

Bambo Tsehaye Tesfamariam anamwalira pa 30 November, 2016 mu mzinda wa Asmara. Iwo anatulutsidwa m’ndende pa 10 September, 2015 chifukwa choti ankadwala kwambiri ndipo sanalandire thandizo loyenera la mankhwala pa nthawi yomwe anali m’ndende. A Tesfamariam anabadwa mu 1941 m’tawuni yotchedwa Nefasit m’dziko la Eritrea. Iwo anasiya mkazi dzina lake Hagosa Kebreab yemwe anamukwatira mu 1973. Anasiyanso ana okwana 7, atsikana 4 ndi anyamata atatu. Iwo anabatizidwa monga wa Mboni za Yehova m’chaka cha 1958.

A Tesfamariam anamangidwa mu January 2009, pa zifukwa zosadziwika bwino ndipo anaikidwa m’ndende ku Meitir Camp. Pa October 5, 2011, a Tesfamariam limodzi ndi a Mboni anzawo 24 amene analinso pa ndendeyo, anaikidwa m’nyumba ya malata okhaokha n’cholinga choti apatsidwe chilango chapadera. Hafu ya nyumbayo inali pansi pa nthaka ndipo anakhala m’nyumbayi mpaka mu August 2012. Ambiri mwa anthuwo anayamba kudwala kwambiri chifukwa choti m’nyumbamo munkatentha kwambiri komanso sankapatsidwa chakudya ndi madzi okwanira.

Chifukwa cha mavuto amene ankakumana nawowa, a Misghina Gebretinsae ndi a Yohannes Haile anafera m’ndendemo pomwe a Kahssay Mekonnen ndi a Goitom Gebrekristos anafa atatulutsidwa. Pambuyo pake a Tesfamariam nawonso anamwalira.