Pitani ku nkhani yake

NOVEMBER 4, 2016
CAMEROON

Ngozi Yoopsa ya Sitima ku Cameroon

Ngozi Yoopsa ya Sitima ku Cameroon

M’mawa wa pa 21 October, 2016,sitima yopita ku Cameroon mumzinda wa Douala, inasiya njanji pafupi ndi tauni ya Eseka, yomwe ili pa mtunda wa makilomita pafupifupi 120 kuchokera ku Yaoundé komwe ndi likulu la dzikoli. Anthu oposa 600 anavulala pangoziyo ndipo ena oposa 70 anafa.

Pa anthu ovulalawo, 16 anali a Mboni za Yehova. Kuonjezera apo, wa Mboni za Yehova mmodzi, yemwe anali ndi zaka 65 komanso anali mkulu mumpingo wa Mboni wa ku Douala, anafa pangoziyo. Ndife achisoni chifukwa cha imfa ya m’bale wathuyu komanso mavuto omwe anthuwa pamodzi ndi abale awo akukumana nawo chifukwa cha ngoziyo.

Lankhulani ndi:

Padziko Lonse: David A. Semonian, Office of Public Information, 1-718-560-5000

Cameroon: Gilles Mba, 237-6996-30727