Pitani ku nkhani yake

Ochititsa Lendi Nyumba Analembera a Mboni za Yehova Makalata

Ochititsa Lendi Nyumba Analembera a Mboni za Yehova Makalata

Posachedwapa, a Mboni za Yehova anamaliza kugwira ntchito yowonjezera maofesi a nthambi ya Wallkill ku New York. Ntchitoyi inatenga zaka 6 ndipo m’zaka ziwiri zomalizira, kunabwera anthu ambiri omwe anadzipereka kudzagwira ntchitoyi. Pofuna kupezera anthu amenewa malo okhala, a Mboni anafunika kuchita lendi nyumba zina kuti anthuwo azikhalamo. Choncho anapeza nyumba 25 kuchokera m’madera ozungulira nthambiyi.

Zomwe Ananena Zokhudza Alendi Awo

Kodi anthu ochititsa lendi ananena zotani zokhudza a Mboni za Yehova omwe ankakhala m’nyumba zawo?

  • Mayi wina analemba kuti: “Ine ndi mwamuna wanga timakhala pafupi ndi nyumba yomwe tinkachititsa lendiyo. Tinkasangalala kwambiri kukhala ndi anthu amenewa. Tinkaona kuti ndi anthu osavuta kuchita nawo zinthu komanso ansangala.”

  • Mayi wina yemwe ankakhalanso pafupi ndi nyumba yomwe ankachititsa lendi analemba kuti: “Tinkakhala nawo bwino kwambiri. Pakhomo pathu tili ndi kadamu kosambiriramo moti anthuwa ankabwera kawirikawiri kudzasambira. Akabwera, ankachita zinthu mwaulemu komanso moganizira ena. Tinkasangalala nawo kwambiri moti tiwasowa.” Mayiwa analembanso kuti: “Sitinakhalepo ndi anthu abwino ngati amenewa.”

  • Wochititsa lendi wina anati: “Zinali zosangalatsa kuti sikuti anangokhala anthu alendi koma tinapanga nawo ubale.”

Zomwe Ananena Zokhudza Mmene Alendiwo Anasamalirira Nyumba Zawo

Kodi anthu ochititsa lendi ananena zotani, alendiwo atachoka?

  • Wochititsa lendi wina yemwe tamutchula kale ananenanso kuti: “Nthawi zonse anthuwa ankapereka ndalama zalendi pa nthawi yake. Ankasamalira bwino nyumba yathu moti pamene amasamuka anaisiya ili bwino.”

  • Anawonjezeranso kuti: “Tikukuthokozani kwambiri a Mboni za Yehova chifukwa chosamalira bwino nyumba yathu. Sitimayembekezera kuti nyumba yathu mungaikonze chonchi.”

  • Mayi wina anafotokoza kuti: “Chifukwa choti timadziwa mmene anthu a m’chipembedzo chanu amachitira zinthu, sitinawauze kuti atipatsiretu ndalama yapadera yoti tidzagwiritse ntchito pokonzetsa nyumbazi zitakhala kuti sanazisamalire bwino. Pamene ankasamuka, anasiyadi nyumba zathu zili bwino.”

  • Nthawi ina a Mboni atakonza zinthu panyumba ina, mwiniwake wanyumbayo anafunsa kuti: “Kodi zingatheke kuti anthu inu ndizikuitanani ndikakhala ndi ntchito inayake? Chifukwa mukalonjeza kuti mumaliza ntchito pa tsiku linalake, mumaimalizadi. Koma anthu ena amene ndimawapatsa ntchito sachita zimenezi.”

Zimene Ananena Posonyeza Kuyamikira

  • Masiku oti walendi wina atuluke m’nyumba atayandikira, mwiniwake wa nyumbayo ananena kuti: “A Mboniwa akanapitiriza kukhala m’nyumbayi ndikanawakomera mtima n’kuwachepetserako ndalama zalendi.”

  • Mwiniwake wa nyumba ina ananenanso kuti: “Pakanakhala mwayi wina, tikanakonda kuchititsanso lendi nyumba yathu kwa a Mboni.”