NYIMBO 156
Ndi Maso a Chikhulupiriro
1. Ndioperenji mkango?
Ndioperenji anthu?
Yehovatu alipo
Ndiopenso chani!
M’lungu andipulumutsa.
(KOLASI)
Ndi masotu a
chikhulupiriro
Sindidzaopa
chilichonsecho.
Yehovatu alipo
Sindichita mantha,
Amakhala nane
pafupi
An’thandiza.
2. Atumiki akale
Anakhulupirika.
Chikhulupiriro
Chinawathandiza.
M’lungu adzawaukitsa.
(KOLASI)
Ndi masotu a
chikhulupiriro
Sindidzaopa
chilichonsecho.
Yehovatu alipo
Sindichita mantha,
Amakhala nane
pafupi
An’thandiza.
(VESI LOKOMETSERA)
Ndi Yehova,
zonse ndi
zotheka.
Ndili n’chikhulupiriro.
Chikhulupiriro
chathandiza kuti
Ndipirire
pa mavuto.
3. M’lungu wandilonjeza
Tsogolo labwino.
Ndipirirebe
Poti posachedwa
Yehova athetsa mavuto.
(KOLASI)
Ndi masotu a
chikhulupiriro
Sindidzaopa
chilichonsecho.
Yehovatu alipo
Sindichita mantha,
Amakhala nane
pafupi
An’thandiza.
An’thandiza.
(Onaninso Aheb. 11:1-40.)