NYIMBO 153
Ndithandizeni Ndikhale Wolimba Mtima
1. Ndilitu ndi mantha
Zinthu zikuvuta.
M’mavuto m’mandithandiza
M’makhala pafupi.
Ndingavutikedi,
Koma ndikudziwa
Ndinu wokhulupirika,
Mudzanditeteza.
(KOLASI)
Yehova, mundithandize
Ndiziona kuti
Ndizothekatu kupirira
Ndilimbedi mtima.
Tili ndi ambiri
Kuposa ’daniwa.
Yehova thandizeni
Muwagonjetsadi.
2. Ndingachite mantha.
Pandekha n’zovuta.
Mumanditeteza ndithu
Ndidalire inu.
Mundithandizetu,
Ndisachite mantha.
Palibe choti ndiope,
M’ndende kaya imfa.
(KOLASI)
Yehova, mundithandize
Ndiziona kuti
Ndizothekatu kupirira.
Ndilimbedi mtima.
Tili ndi ambiri
Kuposa ’daniwa.
Yehova thandizeni
Muwagonjetsadi.
(KOLASI)
Yehova, mundithandize
Ndiziona kuti
Ndizothekatu kupirira.
Ndilimbedi mtima.
Tili ndi ambiri
Kuposa ’daniwa.
Yehova thandizeni
Muwagonjetsadi.
Yehova thandizeni
Muwagonjetsadi.