NSANJA YA OLONDA December 2015 | Kodi N’zotheka Kumvetsa Zimene Baibulo Limanena?

Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti, ‘N’chifukwa chiyani ndimavutika kumva zimene Baibulo limanena?’

NKHANI YAPACHIKUTO

Baibulo Ndi Buku Lothandiza Kwambiri

Anthu ambiri amaona kuti Baibulo ndi buku lofunika, koma sadziwa kuti lingawathandize kwambiri pa moyo wawo.

NKHANI YAPACHIKUTO

Baibulo Ndi Buku Lomveka Bwino

Mfundo 4 zomwe zimasonyeza kuti Baibulo linalembedwa momveka bwino.

NKHANI YAPACHIKUTO

Mukhoza Kumvetsa Zimene Baibulo Limanena

Ngati Baibulo linalembedwa momveka bwino, n’chifukwa chiyani muyenera kuthandizidwa kuti mumvetse zimene limanena?

Kodi Anthu Adzasiya Kuchita Zachinyengo?

Kodi munasiya ndale, chipembedzo kapena bizinezi inayake mutakhumudwa chifukwa cha chinyengo?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Ayuda omwe anapita ku Yerusalemu pa Pentekosite mu 33 C.E., analidi ochokera ‘mu mtundu uliwonse wa pansi pa thambo’? Kodi anthu amene ankapita ku zikondwerero ku Yerusalemu ankagona kuti?

Kodi N’zoona Kuti Petulo Anali Papa Woyamba?

Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti: “Ndikukuuza kuti, Iwe ndiwe Petulo, ndipo pathanthwe ili ndidzamangapo mpingo wanga”?

ZIMENE OWERENGA AMAFUNSA

Kodi Cholakwika N’chiyani Ndi Miyambo Yomwe Imachitika pa Khirisimasi?

Miyambo yomwe imachitika pa Khirisimasi ndi yachikunja. Kodi pali vuto lililonse kuchita miyambo imeneyi?

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi N’zotheka Kumudziwadi Mulungu?

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Sayansi Imagwirizana ndi Baibulo?

Kodi m’Baibulo muli mfundo zolakwika zokhudza sayansi?