NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) May 2013

Magaziniyi ikufotokoza mmene tingagwirire ntchito yathu yolalikira. Ikufotokozanso makhalidwe amene angatithandize kuti tizilankhulana bwino komanso tizisangalala m’banja.

Muzigwira Bwino Ntchito Yanu Yolalikira

N’chifukwa chiyani zili zofunika kwambiri kuti anthu amve uthenga wabwino? Nanga tingatani kuti tikwanitse kugwira ntchito yathu monga alaliki?

Kodi Ndinu “Odzipereka pa Ntchito Zabwino”?

Magaziniyi ikufotokoza mmene anthu angayambire kulambira Mulungu chifukwa choona kudzipereka kwathu pa ntchito yolalikira komanso khalidwe lathu labwino.

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kale anthu a mitundu yambiri ankapha anthu opalamula milandu ina powapachika pamtengo. Koma kodi Aisiraeli ankachitanso zimenezi?

Muzilankhulana Bwino Kuti Banja Lanu Likhale Lolimba

Kulankhulana bwino n’kofunika kwambiri kuti banja likhale losangalala. Nkhani ino ikufotokoza makhalidwe omwe angatithandize kuti tizilankhulana bwino.

Makolo ndi Ana Ayenera Kulankhulana Mwachikondi

Makolo ndi ana ayenera kulankhulana mwachikondi

MBIRI YA MOYO WANGA

Zimene Zatithandiza Kukhalabe Osangalala

Patricia ali ndi ana awiri omwe amadwala matenda enaake obadwa nawo. Werengani kuti mudziwe zimene zawathandiza kukhalabe osangalala ngakhale kuti akukumana ndi mavuto amenewa.

Muzisankha Zinthu Mwanzeru Kuti Musataye Madalitso Anu

Kodi Akhristu ali ndi madalitso otani, nanga kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Esau?

KALE LATHU

Anakhalabe Okhulupirika pa “Ola la Kuyesedwa”

Werengani kuti mudziwe mmene anthu anachitira chidwi ndi Ophunzira Baibulo chifukwa chosalowerera nkhondo pa nthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse mu 1914.