NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) March 2013

Magaziniyi ikukumbutsa Akhristu onse zimene angachite kuti apitirizebe kuthamanga pa mpikisano wokapeza moyo wosatha. Ikufotokozanso zimene tingachite kuti tidziwe mtima wathu komanso kudziwa Mulungu wathu, Yehova.

Anthu Okonda Yehova ‘Alibe Chowakhumudwitsa’

Kodi Baibulo limatanthauza chiyani likamanena kuti anthu amene amakonda malamulo a Yehova alibe chowakhumudwitsa? Werengani kuti mudziwe zimene mungachite kuti mupirire pa mpikisano wokapeza moyo wosatha.

Kodi Muli Ndi “Mtima Wodziwa” Yehova?

Mawu a mneneri Yeremiya angakuthandizeni kuti mtima wanu wophiphiritsa ukhale wathanzi.

Popeza “Mwadziwa Mulungu,” Kodi Muyenera Kuchita Chiyani?

Werengani kuti mudziwe chifukwa chake tiyenera kumadzifufuza kawirikawiri kuti tidziwe ngati chikhulupiro chathu chidakali cholimba komanso ngati tidakali odzipereka kwa Yehova Mulungu.

Tizitonthozana

Aliyense anadwalapo ndipo ena anadwala mwakayakaya. Tikakumana ndi mavuto ngati amenewa, kodi tingatani kuti tipirire?

Yehova Ndi Malo Athu Okhalamo

N’chifukwa chiyani sitikayika kuti Yehova adzateteza anthu ake ngakhale kuti tikukhala m’dziko loipa?

Muzilemekeza Dzina Lalikulu la Yehova

Kodi inuyo mumaona bwanji mwayi wanu wogwiritsa ntchito dzina la Yehova? Kodi kudziwa komanso kuyenda m’dzina la Mulungu kumatanthauza chiyani?

Kodi Josephus Analembadi Zimenezi?

Kodi Myuda wina wolemba mbiri dzina lale Flavius Josephus ndi amene analembadi zimenezi?

Musataye Mtima!

Musamataye mtima n’kumaganiza kuti munthu amene mumamkonda kapena munthu winawake sangaphunzire choonadi. Werengani kuti mudziwe za ena omwe anataya mtima komanso chifukwa chake.