Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mlandu Unatikomera ku Khoti Lalikulu ku Ulaya

Mlandu Unatikomera ku Khoti Lalikulu ku Ulaya

Mlandu Unatikomera ku Khoti Lalikulu ku Ulaya

PA JANUARY 11, 2007, Khoti Loona za Ufulu Wachibadwidwe ku Ulaya (European Court of Human Rights) mumzinda wa Strasbourg, ku France linapereka chigamulo chimene onse ogamulawo anagwirizana nacho. Chigamulocho chinali chokomera Mboni za Yehova za ku Russia pamlandu wapakati pa Mbonizo ndi akuluakulu a boma ku Russia. Chigamulocho chinali choti Mboni za Yehova zipitirirebe kukhala ndi ufulu wopembedza ndiponso woweruzidwa mwachilungamo. Tiyeni tione chimene chinatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke mnyanga.

Mumzinda wa Chelyabinsk, ku Russia, muli mpingo wina wa Mboni za Yehova womwe uli ndi anthu ambiri osamva ndi osalankhula kuposa akumva. Anthu a mumpingowu anachita lendi holo ya koleji inayake yomwe ankachitiramo misonkhano. Ndiye Lamlungu pa April 16, 2000, misonkhano yawo inasokonezedwa ndi mayi wina. Mayiyu ndi wapampando wa bungwe loona za ufulu wachibadwidwe m’dzikolo. Iyeyu anali ndi akuluakulu awiri apolisi komanso ndi munthu wina. Chifukwa choti anthuwa, makamaka mayiyo, ankadana ndi Mboni, anaimitsa msonkhanowo ponamizira kuti unali wosaloledwa mwalamulo. Motero, pa May 1, 2000, Mboni za Yehova zinaletsedwa kusonkhana mu holoyo.

Mbonizo zinakadula chisamani kwa mkulu woona zamalamulo mumzindawo koma zimenezi sizinaphule kanthu. Malamulo oyendetsera dziko la Russia ndiponso a bungwe loona za ufulu wa anthu (Convention for the Protection of Human Rights and Fundamental Freedoms) amapereka ufulu wopembedza ndi kusonkhana. Choncho Mbonizo zinadula chisamani kukhoti laling’ono ndipo zitalephera kumeneku zinakatula mlanduwo kukhoti lalikulu pochita apilo. Mlandu umenewu usanayambike n’komwe, pa July 30, 1999, khoti lalikulu kwambiri m’dzikolo linazenga mlandu wina n’kugamula kuti, “malingana ndi malamulo a dziko la Russia okhudza ufulu wopembedza ndi kusonkhana, mawu oti kupembedza ndi kusonkhana ‘mosasokonezedwa’ amatanthauza kuti, palibe chifukwa chokapemphera chilolezo kwa akuluakulu aboma kuti muchite mwambo winawake wachipembedzo pamalo ovomerezeka mwalamulo.” Chigamulochi chikanathanso kugwira ntchito pamlandu watsopanowu kukhoti laling’ono ndi lalikulu lija, koma sizinatero ayi.

Motero pa December 17, 2001, mlanduwu anapita nawo ku Khoti Loona za Ufulu Wachibadwidwe ku Ulaya. Tsiku lomva mlandu linali September 9, 2004. Mfundo zotsatirazi ndi zina mwa mfundo za m’chigamulo chimene khotili linapereka:

“Khoti lino lapeza kuti odandaulawa anawaphwanyira ufulu wawo wopembedza, chifukwa choti pa 16 April 2000, akuluakulu aboma anaimitsa misonkhano yawo.”

“Panalibiretu chifukwa chogwirizana ndi lamulo choti asokonezere msonkhano wachipembedzowu, womwe unkachitidwa pa malo omwe amachitapo lendi movomerezeka n’cholinga choti azisonkhanapo.”

“[Khoti lino] laonanso kuti m’mbuyo monsemu Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia lakhala likugamula kuti, pofuna kuchita misonkhano yachipembedzo, simufunikira kupempha chilolezo kwa akuluakulu oimira boma kapena kuyamba kaye mwawadziwitsa.”

“Motero posokoneza msonkhano wa odandaulawa pa 16 April 2000, wapampandoyo ndi anzake anaphwanya Sekishoni 9 [yonena za ufulu wopembedza] ya malamulo a bungwe loona za ufulu wa anthu.”

“Khoti lino lapeza kuti makhoti a ku Russia sanakwanitse udindo wawo . . . woonetsetsa kuti mlandu wa odandaulawa wazengedwa mosakondera. Makhotiwa aphwanya Sekishoni 6 [yonena za ufulu woweruzidwa mwachilungamo] ya malamulo a bungwe loona za ufulu wa anthu.”

Mboni za Yehova zimayamikira Mulungu kwambiri chifukwa chowathandiza kuti mlandu wawo kukhoti loona za ufulu wachibadwidwe ku Ulaya uwakomere. (Salmo 98:1) Kodi zimene khotili linagamula zikhudza mayiko ochuluka bwanji? Joseph K. Grieboski, yemwe ndi mkulu wa bungwe lina loona za kupembedza ndi kupanga malamulo, anati: “Ichi ndi chigamulo chofunika kwambiri chomwe chilimbikitse zedi ufulu wopembedza ku Ulaya konse, chifukwa choti chikhudza mayiko onse amene ali pansi pa Khoti Loona za Ufulu Wachibadwidwe ku Ulaya.”