Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mtengo “Wolira” ndi “Misozi” Yake Imene Imagwira Ntchito Zosiyanasiyana

Mtengo “Wolira” ndi “Misozi” Yake Imene Imagwira Ntchito Zosiyanasiyana

 Mtengo “Wolira” ndi “Misozi” Yake Imene Imagwira Ntchito Zosiyanasiyana

‘Tengani mankhwala a vunguti kuti muthetse kuwawa,’ limatero lemba la Yeremiya 51:8, NW. Kufufuza gwero lina la mankhwala ochepetsa ululu ndiponso ochiritsa ameneŵa kukutitengera ku chilumba cha Chios chomwe chili m’nyanja ya Aegean.

KUCHIYAMBI kwa chilimwe, alimi a pachilumba chimenechi amakonzekera kukolola mwa njira yodabwitsa kwambiri. Amasesa pansi pa mitengo yobiriŵira yonga zitsamba imene amaitcha mitengo ya mastic ndipo akatero, amazira pansipo ndi dothi loyera. Ndiyeno alimiwo amacheka makungwa ake, zimene zimachititsa kuti mitengoyo “ilire.” “Misozi” ya chikasu ya utomoni kapena kuti mambidza imayamba kutuluka. Pakatha milungu iŵiri kapena itatu, madontho a utomoniwo amaundana ndipo alimiwo amaututa, mwina pa thunthu pomwepo kapena padothi pamene anazira paja. “Misozi” imeneyi imene amaitcha gum mastic, yagwiritsidwa ntchito kupangira bvunguti.

Komabe asanakolole, pamafunika kuleza mtima ndiponso kugwira ntchito zolimba. Thunthu lotuwa la mitengoyi lomwe ndi lopiringidzika limakula pang’onopang’ono. Pamatenga zaka 40 kapena 50 kuti mtengowo ukhwime, ndipo ukakhwima kutalika kwake ndi mamita aŵiri kapena atatu okha basi.

Kuwonjezera pa ntchito yaikulu yotema thunthu ndi kututa ‘misoziyo,’ pamafunikanso ntchito yaikulu kuti apange utomoni wonunkhira. Alimi akatuta “misozi” ya mtengo wa mastic, amaisefa, kuitsuka ndi kuiika m’magulu malinga ndi kukula kapena kuoneka bwino kwake. Kenako utomoni wonunkhirawo amauyeretsa ndipo tsono angathe kuugwiritsa ntchito zosiyanasiyana.

Mbiri ya Mtengo Wofunika Kwambiri Umenewu

Liwu la Chigiriki lakuti “mastic” ndilogwirizana ndi liwu lotanthauza kuti “kukukuta mano.” (Mateyu 8:12) Dzina limeneli likusonyeza kuti mwina kuyambira kale, utomoni wa mitengo ya mastic ankaugwiritsa ntchito ngati chingamu kuti azitulutsa mpweya wabwino.

Nkhani yakale kwambiri yonena za mitengo ya mastic analemba ndi Herodotus yemwe anali wolemba mbiri wa Chigiriki wa m’zaka za m’ma 400 B.C.E. Olemba mabuku ndi madokotala ena akale​—kuphatikizapo Apollodorus, Dioscorides, Theophrastus, ndi Hippocrates​—anatchulapo zoti utomoni wa mitengo ya mastic unalinso mankhwala. Ngakhale kuti mitengo ya mastic imamera kugombe lonse la nyanja ya Mediterranean, kuyambira cha m’ma 50 C.E., ulimi wa mastic wakhala ukuchitika makamaka ku chilumba cha Chios basi. Anthu amene analanda chilumba cha Chios, kuyambira ndi Aroma kenako Genoa ndiyeno a Ottoman, anatero chifukwa chofuna utomoni wa mastic.

Utomoni wa Mastic Umagwira Ntchito Zosiyanasiyana

Madokotala a kale a ku Igupto ankagwiritsa ntchito utomoni wa mitengo ya mastic kuchiritsa nthenda zosiyanasiyana kuphatikizapo matenda otsekula m’mimba ndi nyamakazi. Ankagwiritsanso ntchito monga  mankhwala ofukizira ndi kukonzera mitembo kuti isawonongeke. Mitengo ya mastic iyenera kuti inali gwero lina la ‘vunguti wa Gileadi,’ umene unadziŵika m’Baibulo kuti unali mankhwala ndiponso kuti unkagwiritsidwa ntchito popanga mafuta odzola ndi pokonza mitembo kuti isawonongeke. (Yeremiya 8:22; 46:11) Ena anena kuti mitengo imene imatulutsa natafi, omwe ndi ena mwa mankhwala amene ankasakaniza kupanga zofukiza zopatulika zimene ankazigwiritsa ntchito popereka nsembe basi, iyenera kuti ili m’gulu la mitengo ya mastic.​Eksodo 30:34, 35.

Lerolino, utomoni wa mitengo ya mastic amakonzera vanishi amene amateteza zithunzi zojambula ndi oilo, mipando, ndiponso zida zoimbira. Amaugwiritsanso ntchito monga zokutira zitsulo ndiponso zoteteza zipangizo zina kuti madzi asaloŵe m’kati mwake. Ndiponso akuti ndi mankhwala abwino kuposa ena aliwonse othandiza kuti mitundu ya mankhwala amene amagwiritsa ntchito popanga zovala ndiponso mitundu ya penti amene ojambula zithunzi amagwiritsa ntchito isasuluke. Utomoni wa mitengo ya mastic augwiritsanso ntchito kumatira zinthu ndiponso pofufuta zikopa. Augwiritsanso ntchito kupangira sopo, mafuta odzola ndi zonunkhiritsa chifukwa cha fungo lake lokoma ndi zina zotero.

Mabuku okwana 25 padziko lonse amene amandandalika mitundu ya mankhwala, afotokozanso za utomoni wa mitengo ya mastic. Utomoniwu akuugwiritsabe ntchito kaŵirikaŵiri monga mankhwala azitsamba ku mayiko a Aluya. Utomoni wa mastic amaugwiritsanso ntchito kupanga zomatira mano ndiponso zokutira m’kati mwa mankhwala a kapisozi.

Monga gwero la vunguti, “misozi” yogwira ntchito zosiyanasiyana ya mtengo “wolira” wa mastic, yachepetsa ululu ndi kuchiritsa matenda kwa zaka zambirimbiri. Ndiyetu m’pake kuti ulosi wa Yeremiya unati: ‘Mutengere zowawa vunguti.’

[Zithunzi patsamba 31]

Chios

Kukolola utomoni wa mastic

“Misozi” ya mitengo ya mastic amaituta mosamala

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi cha Chios ndi chithunzi chosonyeza kukolola: Mwachilolezo cha Korais Library; zithunzi zina zonse: Kostas Stamoulis