Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungayandikire kwa Mulungu Wosaoneka?

Kodi Mungayandikire kwa Mulungu Wosaoneka?

Kodi Mungayandikire kwa Mulungu Wosaoneka?

Mungafunse kuti, ‘Ndingapange motani ubwenzi wolimba ndi munthu amene sindingathe kumuona?’ Limenelo lingaoneke ngati funso logwira mtima. Koma talingalirani:

KODI kuona n’kofunika motani popanga ubwenzi wachikondi ndi wokhalitsa? Kodi mikhalidwe yosaoneka si imene ili yofunika kwambiri? N’njofunikadi! Pachifukwa chimenecho anthu ena apanga ubwenzi wamphamvu ndi anzawo mwa kulemberana makalata nthaŵi zonse, m’makalatamo akumatchula moona mtima zinthu zomwe amakonda, zomwe sakonda, zolinga zawo, makhalidwe awo, nthabwala zawo, ndi mikhalidwe ina.

Anthu akhungu nawonso amasonyeza kuti kuona si kofunika kwenikweni popanga ubwenzi wolimba ndi anthu ena. Lingalirani chitsanzo cha Edward ndi Gwen, mwamuna ndi mkazi wake omwenso ndi akhungu. * Edward anakumana ndi Gwen kusukulu ya anthu akhungu, komwe onseŵa anali kuphunzira. Anakopeka ndi mikhalidwe ya Gwen, makamaka kuona mtima kwake polankhula ndi m’makhalidwe, komanso maganizo ake abwino pa ntchito. Koma Gwen anati iye anakopeka ndi Edward chifukwa chakuti, “Edward anali kusonyeza mikhalidwe yonse imene kuyambira ubwana wanga, ndakhulupirira kuti ndiyo yofunika.” Anatomerana, ndipo patatha zaka zitatu anakwatirana.

“Ngati muli limodzi,” anatero Edward, “khungu silingakulepheretseni kupalana ubwenzi ndi munthu wina. Simungathe kuonana, koma malingaliro n’ngosavuta kuwazindikira.” Lerolino, pambuyo pa zaka 57, akukondanabe kwambiri. Iwo anafotokoza kuti chinsinsi cha ubwenzi wawo wosiririkawo chimakhudza pafupifupi zinthu zinayi: (1) kuzindikira mikhalidwe ya munthu winayo, (2) kulingalira za mikhalidwe imeneyo ndi kukopeka nayo, (3) kulankhulana kwabwino nthaŵi zonse, ndi 4) kuchitira zinthu limodzi.

Mfundo zinayi zimenezi n’zofunika kwambiri pa ubwenzi uliwonse wabwino, kaya ukhale wa mabwenzi wamba, anthu okwatirana kapena ubwenzi wofunika koposa wa pakati pa anthu ndi Mulungu. M’nkhani yotsatira, tidzaona momwe kugwiritsa ntchito mfundo zimenezi kungatithandizire kupanga ubwenzi wolimba ndi Mulungu, ngakhale kuti sitingathe kumuona. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Mayinawo tawasintha.

^ ndime 6 Mosiyana ndi ubwenzi wapakati pa anthu, ubwenzi ndi Mulungu n’ngwozikika pa chikhulupiriro cha kukhalapo kwake. (Ahebri 11:6) Kuti mumve zambiri zokhudza kulimbitsa chikhulupiriro mwa Mulungu, chonde onani buku lakuti, Is There a Creator Who Cares About You?, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.