NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) November 2018

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa December 31, 2018 mpaka February 3, 2019.

“Gula Choonadi Ndipo Usachigulitse”

Kodi kugula choonadi kumatanthauza chiyani? Kodi tikachipeza tiyenera kuchita chiyani kuti tisachigulitse?

“Ndidzayenda M’choonadi Chanu”

Kodi tingatani kuti tisagulitse choonadi chamtengo wapatali chimene Yehova watiphunzitsa?

Muzikhulupirira Yehova Kuti Mukhale ndi Moyo

Buku la Habakuku lingatithandize kukhalabe wodekha pamene takumana ndi mavuto.

Kodi Mumayendera Maganizo a Ndani?

Kodi mungatani kuti muziyenda maganizo a Mulungu osati a anthu?

Tiziyendera Maganizo a Yehova

Kodi tingatani kuti ‘tisinthe maganizo’ athu?

Kukoma Mtima Ndi khalidwe Limene Limasonyezedwa M’mawu ndi Zochita

Kukoma mtima ndi khalidwe limene mzimu wa Mulungu umatulutsa. Kodi tingatani kuti tikhale okoma mtima?

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi anthu Opereka zabwino amene Yesu anawatchula anali ndani, nanga n’chifukwa chiyani anapatsidwa dzina limeneli?

Kodi Ndingapereke Chiyani kwa Yehova?

Kodi ‘zinthu zamtengo wapatali’ zotchulidwa pa Miyambo 3:9 ndi ziti, nanga tingazigwiritse ntchito bwanji kuti zithandize pa zinthu zokhudza kulambira?