Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MFUNDO ZOTHANDIZA AMENE AFEREDWA

Kuvutika Maganizo Chifukwa Choferedwa

Kuvutika Maganizo Chifukwa Choferedwa

A Kostas ananena kuti: “Ine ndi Sophia * tinakhala m’banja zaka zoposa 39 kufikira pomwe Sophia anadwala kwa nthawi yaitali mpaka kumwalira. Mkazi wanga atamwalira, anzanga anandithandiza kwambiri komanso ndinkayesetsa kudzitangwanitsa ndi zinthu zina. Komabe ndinavutika kwambiri ndi chisoni kwa chaka chathunthu. Nthawi zina ndinkasangalala koma mosadziwika bwino ndinkangopezeka kuti ndakhumudwa. Ngakhale kuti padutsa zaka zitatu, nthawi zina ndimavutikabe maganizo.”

Kodi munaferedwapo? Ngati zinakuchitikiranipo, mwina mungamvetse mmene a Kostas amamvera. Kumwalira kwa mwamuna kapena mkazi wako, wachibale kapena mnzako, kumasokoneza maganizo kwambiri. Akatswiri ofufuza zomwe zimachitika munthu akaferedwa, amavomerezanso kuti zimenezi si zachilendo. Magazini ina inanena kuti: “Anthu akaferedwa munthu amene ankamukonda kwambiri, amamva kuti ataya munthu wofunika amene sadzamuonanso ndipo zimenezi zimawapweteka mumtima.” (The American Journal of Psychiatry) Chifukwa chovutika maganizo mwina mungamadzifunse kuti: “Kodi zinditengera nthawi yaitali bwanji ndikumva chonchi? Kodi ndingadzakhalenso wosangalala? Nanga ndingatani kuti ndisamavutike ndi maganizo?”

Magaziniyi ikuyankha mafunso amenewa. Nkhani yotsatirayi ikufotokoza zimene mungakumane nazo ngati munthu amene munkamukonda anamwalira chaposachedwapa. Nkhani zina za m’magaziniyi zikufotokoza njira zomwe mungatsatire kuti muchepetseko chisoni.

Tikukhulupirira kuti mfundo za m’magaziniyi, zikhala zolimbikitsa kwa aliyense amene akuvutika maganizo chifukwa choferedwa.

^ ndime 3 Maina ena asinthidwa.