Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Musamadzipanikize Kwambiri ndi Ntchito

Musamadzipanikize Kwambiri ndi Ntchito

Musamadzipanikize Kwambiri ndi Ntchito

POPEZA kuti padzikoli pali mavuto aakulu a zachuma, anthu ambiri amafunitsitsa atakhala pantchito yodalirika yomwenso ingawathandize kupeza ndalama zokwanira kuti azitha kusamalira banja lawo. Koma kupeza ntchito yodalirika n’kovuta, makamaka panopa chifukwa anthu ambiri akuchotsedwa ntchito. Komabe ngati ntchito yakutherani mwadzidzidzi, mungafunike kufufuzanso ina mwakhama.—Onani bokosi patsamba 8 ndi 9.

Komabe, dziwani kuti pali zinthu zinanso zofunika kwambiri kuposa ntchito. Bambo wina wapabanja, dzina lake Glenn, yemwe amakhala ku Australia, anati: “Kunena zoona, palibe munthu amene atatsala pang’ono kufa anganene kuti, ‘Ndikulakalaka ndikanati ndiziweruka mochedwa kuntchito.’” N’zoona kuti kugwira ntchito molimbika kumathandiza kuti munthu akhale ndi moyo wosangalala. Komabe, pali zinthu zinanso zofunika kuti munthu akhale wosangalala, monga kucheza ndi banja lake, kukhala ndi nthawi yopuma ndiponso yochita zinthu zauzimu. Kodi mungatani kuti muzikhala ndi nthawi yochita zinthu zofunika zimenezi?

Muzikhala ndi Nthawi Yopuma

Baibulo limatiuza kuti kugwira ntchito molimbika n’kofunika kuti tizisamalira mabanja athu. (Aefeso 4:28) Koma limatiuzanso kuti ‘tidye, timwe ndi kuona zabwino m’ntchito zathu zonse.’ (Mlaliki 3:13) Kugwira ntchito nthawi yaitali popanda kupuma mokwanira kungachititse kuti musamasangalale komanso mudwale matenda osiyanasiyana.

Kugwira ntchito nthawi yaitali kungabweretse mavuto monga kunenepa kwambiri, uchidakwa, matenda a mtima, kuchita ngozi pogwira ntchito, nkhawa, kutopa, kuvutika maganizo, kumangokhalira kumwa mankhwala, ndi mavuto ena ambiri. Ndiponso munthu akhoza kufa chifukwa chogwira ntchito kwambiri. Lipoti lina linanena kuti ku Japan pafupifupi anthu 10,000 amafa chaka chilichonse chifukwa chogwira ntchito kwambiri. Chiwerengero chimenechi n’chofanana ndi cha anthu amene amafa pa ngozi zapamsewu m’dzikolo chaka chilichonse. Vuto limeneli, lomwe ku Japan amalitchula kuti karoshi, kutanthauza “kufera pantchito,” lilinso m’mayiko ambiri.

Baibulo limapereka malangizo anzeru awa: “Dzanja limodzi lodzala pali mtendere liposa manja awiri oti tho pali vuto ndi kungosautsa mtima.” (Mlaliki 4:6) Choncho, kugwira ntchito mosapitirira malire n’kofunika. Musamalole kuti ntchito izikudyerani nthawi yanu yonse. Muzisamalira thanzi lanu mwa kukhala ndi nthawi yopuma ndiponso yosangalala ndi ntchito ya manja anu.

Bambo wina dzina lake Andrew, yemwe ali ndi ana atatu, anati: “Tizigwira ntchito kuti tikhale ndi moyo, osati kukhala ndi moyo kuti tizigwira ntchito.” Kukhala ndi nthawi yopuma komanso yosangalala n’kofunikanso kuti mudziwe zimene banja lanu likufunikira. Koma zimenezi n’zovuta, makamaka ngati mukufunikira ndalama zoti mulipirire zinthu zina ndi zina.

Muzikhalanso ndi Nthawi Yocheza ndi Banja Lanu

Mabanja ambiri masiku ano amakhala ndi zochita zambiri ndipo sakhala ndi nthawi yocheza. Mayi wina wa ku England anadandaula kuti: “Ndikamaweruka kuntchito ndimakhala nditatoperatu ndipo nthawi zambiri sindikwanitsa kucheza ndi ana anga.” Ku United States, wachinyamata mmodzi pa achinyamata asanu alionse atafunsidwa, ananena kuti vuto lawo lalikulu ndi lakuti “makolo awo sacheza nawo nthawi yaitali.” Lipoti lina m’dziko lomweli linanena kuti pa avereji mabanja amene mwamuna ndi mkazi ali pantchito, amalankhulana mphindi 12 zokha patsiku.

Chifukwa choona kuti akupanikizika, anthu ambiri akusiya ntchito yawo n’kuyamba ina kuti azikhala ndi nthawi yochitanso zinthu zina. Mwachitsanzo, bambo wina wa ana awiri, dzina lake Timothy, anati: “Ndikaweruka kuntchito ndinkagwiranso ntchito ina kwa maola angapo ndipo mkazi wanga ankagwira ntchito Loweruka ndi Lamlungu. Nthawi zambiri sitinkaonana. Kenako tinaona kuti tikupanikizika ndipo tinayamba ntchito ina. Panopa ine ndi mkazi wanga tikusangalala kwambiri.” Munthu winanso, dzina lake Brian, yemwe anali bwana pasitolo ina anati: “Mkazi wanga ali ndi pakati pa mwana wachiwiri, ndinayamba kufunafuna ntchito yomwe ikanandipatsa mpata wosamalira banja langa. Kenako ndinapeza ntchito ya malipiro ochepa ndi madola 10,000 pachaka kuyerekeza ndi ntchito yanga yoyamba kuti ndizikhala ndi nthawi yambiri yosamalira banja langa, ndipo zimenezi zinathandiza kwambiri.” Mayi wina, dzina lake Melina, anasiya ntchito atabereka mwana wake woyamba. Iye anati: “Zinali zovuta kumangodalira ndalama zimene mwamuna wanga ankalandira. Komabe, tinaona kuti ndi bwino kuti ndisamagwire ntchito, n’cholinga choti ndizisamalira mwana wathu Emily m’malo mokamusiya kumalo osamalirira ana.”

Komabe, tisaiwale kuti mabanja ambiri amapeza ndalama movutikira. M’mabanja ena, mwamuna kapena mkazi amagwira ntchito ziwiri kapenanso onse awiri amapita kuntchito, kusiya ana ali ndi agogo awo kapena kukawasiya kumalo osamalira ana.

Inunso mungapeze njira zina zokuthandizani kuti muzikhala ndi mpata wosamalira banja lanu. Mfundo yaikulu ndi yakuti: Musamalephere kusangalala ndi banja lanu chifukwa chokonda kwambiri ntchito.

Dziwani kuti ngati mutakhala ndi nthawi yogwira ntchito, yopuma ndiponso yocheza ndi banja lanu, mudzapindula kwambiri. M’nkhani yotsatira, tiona chinthu china chofunika kwambiri chimene chingakuthandizeni kuti mukhale ndi moyo wosafuna zambiri koma wosangalala.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Musamalole kuti ntchito izikudyerani nthawi yanu yonse

[Mawu Otsindika patsamba 5]

“Dzanja limodzi lodzala pali mtendere liposa manja awiri oti tho pali vuto ndi kungosautsa mtima.”—Mlaliki 4:6.

[Mawu Otsindika patsamba 6]

Musamalephere kusangalala ndi banja lanu chifukwa chokonda kwambiri ntchito

[Bokosi/Chithunzi patsamba 6]

KODI MUNGASANKHE CHIYANI PAKATI PA NTHAWI NDI NDALAMA?

Akatswiri ena a zaka za m’ma 1900 ankakhulupirira kuti zipangizo zamakono zingathandize kuti anthu asamapanikizike ndi ntchito ndiponso kuti “azikhala ndi nthawi yaitali yosangalala.”

Chakumayambiriro kwa m’ma 1930, Pulofesa Julian Huxley ananena kuti m’tsogolo palibe munthu amene azidzagwira ntchito masiku opitirira awiri pa mlungu. Munthu wina wa bizinesi, dzina lake Walter Gifford ananena kuti zipangizo zamakono “zithandiza aliyense kukhala ndi mpata wochita zinthu zina . . . , ndiponso wokhala ndi nthawi yosangalala.”

Nanga bwanji pa nkhani yokhala ndi chuma? Katswiri wina wophunzira za chikhalidwe cha anthu, dzina lake Henry Fairchild, ananena monyadira kuti zimenezi zithandiza kuti mafakitale azipanga “katundu wambiri kuposa amene anthu angafune, ndipo anthu azigwira ntchito . . . maola anayi okha.”

Koma kodi zimene anthuwa ananena zachitikadi? Mayiko atukuka kwambiri m’zaka za m’ma 1900 ndi m’ma 2000 ndipo zimenezi zinayenera kuthandiza kuti anthu asamapanikizike kwambiri ndi ntchito. Koma kodi chachitika n’chiyani? Munthu wina, dzina lake John de Graaf, analemba kuti: “[Anthu] akuona kuti kubwera kwa zipangizo zamakono n’kothandiza kuti apeze ndalama ndiponso katundu wambiri, koma osati kupeza nthawi yambiri yopuma. Kunena mwachidule, tingati anthu asankha kukhala ndi ndalama zambiri, m’malo mokhala ndi nthawi yopuma.”