Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Makolo Mungathandize Bwanji Ana Anu?

Kodi Makolo Mungathandize Bwanji Ana Anu?

Kodi Makolo Mungathandize Bwanji Ana Anu?

BUNGWE lina la zamaphunziro ku United States, linalimbikitsa ophunzira kuti ‘azidzikakamiza kuchita zinthu zimene zimawavuta.’ Pofuna kukwaniritsa zolinga zawo, achinyamata ambiri amachita zinthu mopitirira muyeso. Madeline Levine, yemwe tamutchula m’nkhani ina ija, anati: “Achinyamata ambiri amapanikizika kwambiri mpaka kudwala chifukwa chakuti amaphunzira zinthu zambiri nthawi yochepa, amachita masewera ambiri, amachita maphunziro owakonzekeretsa za kuyunivesite, ndiponso amaphunzitsidwa ndi aphunzitsi ambiri zedi.” Ophunzira otere sakhala ndi moyo wathanzi.

Ngati mukuona kuti mwana wanu akupanikizika kwambiri kusukulu, muyenera kulankhulana ndi aphunzitsi ake. Auzeni aphunzitsiwo zimene mwaona zokhudza mwana wanuyo. Ndi udindo wanu kuchita zimenezi.

Baibulo limalimbikitsa makolo kuti azisonyeza chidwi pa maphunziro a ana awo. Kale ku Isiraeli, Mose analangiza makolo kuti: ‘Muziphunzitsa malamulo a Mulungu mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.’—Deuteronomo 6:7.

Kukhudzidwa kwambiri ndi maphunziro a mwana wanu, sikulakwa. Zimenezi ndi umboni wakuti mumam’konda. Ndipo zingathandize kuti mwana wanu asamapanikizike kwambiri ndi sukulu.

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Kambiranani ndi aphunzitsi ngati mwana wanu akupanikizika ndi sukulu