Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Zinachitikira Kuti?

1. Kodi ndi mumtsinje uti umene Mose akadali khanda anamupeza?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Eksodo 2:1-10.

Pamapu awa lembani mzere wozungulira yankho lanu.

Firate

Yordano

Nile

▪ Kodi ndani amene ankayang’anira Mose ataima chapatali?

․․․․․

▪ Kodi ndani amene anapeza Mose akuyandama mumtsinje?

․․․․․

▪ Kodi ndani anasankhidwa kuti azilera Mose?

․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi mlongo wa Mose anasonyeza makhalidwe otani? Ngati muli ndi m’bale kapena mlongo wanu, kodi mungamutsanzire bwanji mlongo wa Mose?

Kuchokera M’magazini Ino

Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowa.

TSAMBA 8 Kodi munthu aliyense wochenjera amatani? Miyambo 13:․․․․․

TSAMBA 8 Kodi chingachitike n’chiyani mukamakhala panokha? Miyambo 18:․․․․․

TSAMBA 9 Kodi mayi wabwino amatani? Miyambo 31:․․․․․

TSAMBA 9 N’chifukwa chiyani muyenera kuyesetsa kukhala ndi luso la kulingalira? Miyambo 2:․․․․․

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Kodi mungapeze zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

Ndani Ali M’gulu la Makolo a Yesu?

Onani zokuthandizani kupeza yankho. Onaninso malembawo. Kenaka lembani mayina olondola pa mizereyi.

2. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Ndinakanthidwa ndi khate chifukwa ndinafuna kupereka nsembe yofukiza paguwa la nsembe la Yehova.

Werengani 2 Mbiri 26:16-19.

3. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Ndinali mfumu yabwino ndipo ndinamanga chipata cha kumtunda cha nyumba ya Yehova.

Werengani 2 Mbiri 27:1-4.

4. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Ndinapsereza ana anga nsembe m’Chigwa cha Hinomu.

Werengani 2 Mbiri 28:1, 3, 4.

▪ Mayankho ali pa tsamba 12

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31

1. Nile.

▪ Mlongo wa Mose.

▪ Mwana wamkazi wa Farao.

▪ Mayi a Mose.

2. Uziya.—Mateyo 1:8.

3. Yotamu.—Mateyo 1:9.

4. Ahazi.—Mateyo 1:9.