Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tilikhulupirire Kapena Ayi?

Tilikhulupirire Kapena Ayi?

Tilikhulupirire Kapena Ayi?

“Musamakhulupirire matabwa owola,” analemba choncho William Shakespeare, yemwe anali wolemba masewero wa ku England. Indedi, munthu asanakwere bwato la matabwa, angafunike kuona kaye ngati matabwa ake si owola.

MAWU a Shakespeare amenewa akutikumbutsa zimene mfumu yanzeru Solomo ya ku Isiraeli inanena zaka pafupifupi 3,000 zapitazo. Iye analemba kuti: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.” (Miyambo 14:15) N’zoona kuti wachibwana amangochita zinthu mwachimbulimbuli; amangokhulupirira chilichonse chimene wamva ndiponso sachedwa kutsatira malangizo ndi mfundo zopanda nzeru. Mofanana ndi kukwera bwato la matabwa owola, kukhulupirira zinthu zolakwika kungatiike m’mavuto. Koma mwina mungafunse kuti, ‘Kodi pali malangizo aliwonse amene tiyenera kuwakhulupirira?’

Anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse amakhulupirira kwambiri buku lina lakale, lomwe limatchedwa Baibulo Loyera. Iwo amalidalira kuti liwatsogolere. Amatsatira malangizo ndi mfundo zake pochita zinthu. Kodi tinganene kuti iwowa akwera bwato la matabwa owola? Kuti tiyankhe funsoli tiyenera kuyankha kaye funso lakuti, Kodi pali zifukwa zomveka zokhulupirira Baibulo? Galamukani! yapaderayi ifotokoza zinthu zimene zingathandize kuyankha funso limeneli.

Cholinga cha Galamukani! imeneyi si kukuumirizani kuti mutsatire zikhulupiriro kapena mfundo zinazake zachipembedzo. Cholinga chake ndi kungofotokoza zimene zathandiza anthu ambiri kukhulupirira Baibulo. Mukawerenga nkhani zotsatirazi, muona nokha ngati m’pofunika kukhulupirira Baibulo kapena ayi.

N’zofunika kuti muganizire zimenezi mofatsa. Ndipotu, ngati Baibulo lili ndi malangizo odalirika ochokera kwa Mlengi wathu, ndiye kuti inu ndi banja lanu muyenera kudziwa zimene Baibulolo limanena.

Koma choyamba, titchule kaye zinthu zochititsa chidwi zokhudza Baibulo. Mwina ndi anthu ochepa okha amene angakane zoti Baibulo ndi buku lapaderadi.