Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Nthawi ya Chakudya Imatithandiza Kuti Tizikondana”

“Nthawi ya Chakudya Imatithandiza Kuti Tizikondana”

“Nthawi ya Chakudya Imatithandiza Kuti Tizikondana”

KODI m’banja mwanu mumadyera pamodzi chakudya kamodzi kapena kangapo tsiku lililonse? N’zachisoni kuti m’dziko lotanganidwa kwambiri la masiku anoli, anthu a m’mabanja ambiri sadyera pamodzi, aliyense amadya nthawi yakeyake. Komano, nthawi ya chakudya si nthawi yakudya chabe, chifukwa kudyera pamodzi kumakwaniritsa zinthu zofunikira kwambiri monga kulankhulana momasuka ndi kumangirira banja pamodzi.

Algirdas amakhala m’dziko la Lithuania kumpoto kwa Ulaya, pamodzi ndi mkazi wake Rima komanso ana awo aakazi atatu. Iye akuti: “Ngakhale kuti ndimapita kuntchito ndipo ana anga amapita kusukulu, nthawi zonse timadyera chakudya cha madzulo pamodzi. Pa nthawi ya chakudyayi m’pamene tonsefe timakhala omasuka kunena zomwe zachitika tsiku limenelo, n’kuthandizana maganizo pa zinthu zosiyanasiyana zokhudza mavuto athu, maganizo athu, zimene tikufuna kuchita, zimene timakonda ndi zimene sitikonda. Pa nthawi imeneyi, timakambirananso nkhani zauzimu. N’zachidziwikire kuti nthawi yachakudya imatithandiza kuti tizikondana kwambiri.”

Rima nayenso akuti: “Kuphikira limodzi chakudya ndi ana athu kumatithandizanso kuti tizilankhulana zakukhosi. Ana athu amasangalala tikamagwira nawo ntchito limodzi m’khitchini, ndipo panthawi yomweyomweyo, amakhala akuphunzira ntchito zofunikira. Choncho, timachitira zonse pamodzi, ndipo nthawi ya ntchito imakhalanso nthawi yosangalala.

Algirdas, Rima ndi ana awo akusangalala kwambiri chifukwa chodyera pamodzi chakudya. Ngati banja lanu silidyera pamodzi, bwanji osakonza zoti muzidyera limodzi kamodzi kapena kangapo tsiku lililonse, ngakhale banja lanu lili la kholo limodzi. Khama lanu lingapindule koposa.