Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kusisita Mwana N’kofunika?

Kodi Kusisita Mwana N’kofunika?

Kodi Kusisita Mwana N’kofunika?

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU SPAIN

ANITA, mayi wachitsikana wa ku Nigeria, ankasambitsa mwana wake kenako n’kuyamba kumusisita bwinobwino. Onse awiri, mayi ndi mwana wakeyo, ankasangalala nazo kwambiri. Anita anafotokoza kuti, “Umu ndi mmene amayi ambiri a ku Nigeria kuno amalerera ana awo. Amayi anga ankasisita ineyo ndi alongo anga. Kusisita ndi njira yabwino kwambiri yolimbitsira minofu ya mwana ndiponso kuti thupi lake limasuke. Ndikamasisita mwana wanga, ndimaimba nyimbo ndi kumulankhula, ndipo iye amasangalala kwambiri. Zimakhala zosangalatsa kwambiri!”

Kusisita ana kumachitika m’mayiko ambiri, ndipo kukufalikira ku mayiko ena a Azungu. Malinga n’kunena kwa bungwe loona zosisita ana la ku Spain, kusisita ndi njira yabwino kwambiri yomwe imathandiza kholo kulankhulana ndi mwana mwa kum’khudza. Njira imeneyi imaphatikizapo kusisita bwinobwino mapazi, miyendo, msana, chifuwa, mimba, manja ndi nkhope ya mwana.

Kodi mwana amapeza phindu lotani mukamamusisita? Chinthu chachikulu chomwe amapindulapo n’chakuti amamva kuti amakondedwa. Mwana yemwe wangobadwa kumene amafuna kuti makolo ake azimudyetsa ndi kum’sonyeza chikondi. Popeza kuti munthu amayamba adakali wamng’ono kudziwa akakhudzidwa ndi chinthu, kusisita mwana mwachikondi kumene mayi kapena bambo amachita kumapangitsa mwanayo kuona kuti akukondedwa. Mwanjira imeneyi, mungauze mwana zinthu zambiri. Chotero kusisita kungalimbitse chikondi pakati pa makolo ndi mwana wawo kungoyambira pamene wabadwa.

Kuwonjezera pa kusonyeza chikondi, kusisita mwana kungam’thandize kuti thupi lake limasuke, ndipo zimenezi zingapangitse kuti azigona bwino kwa nthawi yaitali ndiponso kuti asamavute. Anthu ena amanena kuti mukamasisita mwana, mphamvu yake yom’teteza ku matenda imakhala yabwino kwambiri. Ndipo popeza kuti kum’sisita mwana kumamuthandiza kuti azizindikira bwino akakhudzidwa, komanso kuti aziona, ndi kumva bwinobwino, kuyeneranso kuti kumam’thandiza kuti azitha kukumbukira ndiponso kudziwa zinthu.

Zipatala zina nazonso zinafufuzapo kuti zione ubwino wa kusisita mwana. Mwachitsanzo, kafukufuku wina anasonyeza kuti ana obadwa nthawi yawo isanakwane amene ankasisitidwa ankatulutsidwa mwamsanga m’chipatala, masiku asanu ndi awiri ana omwe sanasisitidwe asanatulutsidwe. Ndipo ana omwe ankawasisita anali onenepa kuposa omwe sankawasisita.

N’zoonekeratu kuti si akulu okha amene amapindula akamawasisita. Ndithudi, kusisita ana kumawathandiza pa zinthu zambiri osati kungowathandiza kuti thupi limasuke ayi. Mukamawasisita bwinobwino ndi kuwasekerera iwo amaona kuti akukondedwa.