Nkhani ya Dzina la Mulungu Inabutsa Mkangano

Nkhani ya Dzina la Mulungu Inabutsa Mkangano

Nkhani ya Dzina la Mulungu Inabutsa Mkangano

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU NETHERLANDS

AMENE anatembenuza Baibulo latsopano la m’chinenero cha Chidatchi anabutsa mkangano pakati pa akatswiri a maphunziro a Baibulo komanso anthu wamba. Kodi chinabweretsa mkanganowo n’chiyani? Otembenuzaŵa anaganiza zotchula Mulungu ndi dzina lakuti Heer, kapena kuti Ambuye.

M’mwezi wa December, chaka cha 1998, patangotha milungu yochepa otembenuzaŵa atatulutsa Baibulolo kuti anthu alione, gulu la azimayi la m’bungwe la chiprotesitanti lotchedwa Kerk en Wereld (Chalitchi ndi Dziko), linasonyeza kusagwirizana ndi zimenezi polemba makalata. Kodi anatero chifukwa chiyani? Ankaona kuti mawu akuti “Ambuye” amasonyeza kwambiri kuti munthuyo “n’ngwa mwamuna.” Posapita nthaŵi, magulu enanso achikatolika ndi chiprotesitanti anagwirizana ndi gulu la azimayilo. M’mwezi wa February m’chaka cha 1999, akatswiri atatu a maphunziro anathiriraponso ndemanga ponena kuti zikanakhala bwino akadangosiya mawu a Chiheberi amene amangowalemba kuti YEHOVA. Pasanapite nthaŵi, akatswiri a maphunziro a Baibulo, otembenuza, ndiponso anthu amaphunziro apamwamba a zaumulungu anakumana mumzinda wa Amsterdam kuti akambirane nkhaniyi. Atatha kukambiranako, onse amene analipo anapemphedwa kuti avotere dzina limene angalikonde.

Nyuzipepala yotchedwa Nieuwsblad van het Noorden, m’nkhani ya mutu wakuti “Poopa Mulungu, Tiyeni Tisakangane Chifukwa cha Dzina Lake,” inasimba zotulukapo za votiyo kuti: “Mawu akuti AMBUYE anapeza mavoti asanu ndi aŵiri okha. Komanso ambiri mwa mawu ena amene anthu anawatchula sanapeze mavoti ambiri, ndipo zotsatira zake zinali motere: Mawu akuti Dzina (1), Iyeyo (3), Wachifundo (6), Wosatchulika (7), Wamoyo (10), ndi Wamuyaya (15). Ndipo dzina limene linaposa onse ndi lakuti . . . YEHOVA!” Pa March 15, 2001, komiti yoyang’anira ntchito yotembenuza Baibulo latsopanolo inaganiza zogwiritsa ntchito mawu akuti HEER (AMBUYE) m’zilembo zazikulu zochepetsedwa kuti ndiwo aimire dzina la Mulungu.

Mkangano umenewu ukutsimikizira kuti ngakhale kuti anthu akukonda mayina osiyanasiyana otchulira dzina la Mulungu m’chinenero cha chidatchi, akatswiri a zamaphunziro amavomereza kuti Mulungu ali nalo dzina lakelake lom’tchulira. M’Chiheberi dzinali amalilemba ndi zilembo zinayi izi, יהוה, kapena YHWH. Kodi mabaibulo ena akale komanso a posachedwapa a M’chidatchi anatembenuza bwanji zilembo zimenezi?

M’chaka cha 1762 munthu wina wa chidatchi dzina lake Nicolaas Goetzee anasindikiza Baibulo lina lotchedwa Staten. Patsamba lolongosola za m’Baibulolo panali mawu akuti: “Pazifukwa zazikulu ndiponso zodziŵika bwino, sitinatembenuze dzina loyenera kulikumbukira la Mulungu lakuti YEHOVA.” Anthu ena ophunzira kwambiri a chidatchi, monga Pulofesa Nicolaas Beets ndiponso Petrus Augustus de Genestet agwiritsaponso ntchito dzina lakuti Yehova.

N’zochititsa chidwi kuti Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures * limagwiritsa ntchito dzina lakuti Yehova paliponse poyenerera kutero. Mawu oyamba a m’Baibulo limeneli m’chidatchi amanena kuti Baibulolo “likugwiritsabe ntchito mawu akuti ‘Yehova’ chifukwa chakuti anthu amaŵadziŵa bwino mawuŵa kuyambira kale. Ndiponso mawuŵa sakuthaŵana kwenikweni ndi . . . zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu, YHWH.” Motero Baibulo la New World Translation lathandiza anthu ambiri kudziŵa zoona pa nkhani ya dzina la Mulungu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.