Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mzinda wa mu Africa Umene uli ndi Anthu a Chikhalidwe Chosiyanasiyana

Mzinda wa mu Africa Umene uli ndi Anthu a Chikhalidwe Chosiyanasiyana

Mzinda wa mu Africa Umene uli ndi Anthu a Chikhalidwe Chosiyanasiyana

Yolembedwa Ndi Wolemba Galamukani! Ku South Africa

Mukamayenda mumzinda wa Durban mumaona anthu ovala zinthu zosiyanasiyana zokongoladi! Mutha kuona kuti anthu ambiri, makamaka achinyamata akutengera kuvala kwachizungu. Koma taonaninso kuti azimayi achizulu achikulire avala madiresi awo aatali ndithu ndipo kumitu kwawo avala mipango yokongola. Palinso azimayi achimwenye ovala mikanjo kapena kuti madiresi ndi mathalauza achimwenye. Mukamayandikira kufupi ndi m’mphepete mwanyanja, muona amuna ena achizulu atavala zovala zochititsa chidwi akukoka zikuku. Ndithudi, mzinda wa Durban ndi mzinda wapadera mu Africa, umene uli ndi anthu a chikhalidwe chosiyanasiyana. Kodi mbiri ya mzinda wochititsa chidwiwu n’njotani?

Anthu akhala mu mzinda wa Durban, ku South Africa kwa zaka zosakwana 200. Atsamunda pafupifupi 40 ochokera ku Ulaya anadzakhala kuno mu 1824. Panthaŵiyo ufumu wamphamvu wa Azulu wolamulidwa ndi mfumu yawo yodziŵa nkhondo Shaka, unali kumpoto kwa Durban. Patatha zaka makumi aŵiri, mzinda wa Durban ndiponso madera ena ouzungulira anali m’manja mwa dziko la Britain. M’zaka za m’ma 1800 atsamunda atsopanowo anamenyana kangapo konse ndi Azulu.

M’kati mwa nthaŵiyi atsamunda achingerezi anaona kuti nzimbe zinali kumera bwino m’mphepete mwa nyanja. Pofuna kuti minda yawo ya nzimbe ilimidwe, iwo anaitanitsa anthu kuchokera ku India, dziko lomwenso panthaŵiyo linali kulamulidwa ndi Britain. Pakati pa 1860 ndi 1911, amwenye pafupifupi 150,000 anafika ku Durban. Motero, masiku ano m’kati mwa mzinda wa Durban muli anthu oposa 3 miliyoni, a mbali zitatu zadziko lapansi. Kuli azulu omwe ndi akomweko, amwenye a ku India, ndiponso anthu ochokera ku Britain ndi ku madzulo kwa Ulaya.

Mzindawu uli ndi zinthu zinanso zochititsa chidwi. Monga mmene mukuonera pachithunzipa, mzindawu uli ndi gombe lachilengedwe lotetezeka ku nyanja ya Indian Ocean ndi kamtunda kakatalitali. Malo okongolaŵa ndi aatali koposa mamita 90 ndipo ali ndi zomera zambiri. Tsiku lililonse sitima zazikulu zimadutsa pa gombe lachilengedweli. Buku lotchedwa Discovery Guide to Southern Africa limalongosola kuti mzinda wa Durban uli ndi “gombe lalikulu ndiponso lotanganidwa kuposa magombe ena onse mu Africa, ndipo lili pa nambala 9 padziko lonse. Anthu amene ali patchuti amakopeka ndi malo okongola a m’mphepete mwa nyanja amene ali ku Durban ndiponso madzi ake ofundira bwino amawasangalatsa. Kuli malo abwino kwambiri ochitirako maseŵera okwera mafunde, ndipo anthu amasambira mitima ili m’malo chifukwa chakuti kuli maukonde otetezera nsomba zikuluzikulu zodya anthu.

Anthu okonda Baibulo amachita chidwi ndi mzindawu pachifukwa chinanso. Ophunzira Baibulo, monga mmene Mboni za Yehova zinkadziŵikira kale, anakhazikitsa ofesi yanthambi mumzindawu m’chaka cha 1910. Kenaka m’mwezi wa April mu 1914, msonkhano woyamba waukulu wa Ophunzira Baibulo mu Africa unachitikira ku Durban. Anthu okwana 50 anabwera pamsonkhanowu, kuphatikizaponso nthumwi zochokera m’madera akutali a ku South Africa. Pamsonkhano wotchuka umenewu anthu opembedza atsopano 16 anabatizidwa. Anthu angapo amene anali pamsonkhanowu anali Akristu odzozedwa amene anakhulupirika mpaka imfa, ndipo wina mwa anthuwo anali William W. Johnston, amene anali woyamba kuyang’anirapo nthambi mu Africa.

Mboni za Yehova zakhala zikuchita misonkhano yambiri ku Durban chiyambire 1914. Mwezi wa December chaka cha 2000, pafupifupi anthu 14,848 anafika pamisonkhano iŵiri yachigawo ya “Akuchita Mawu a Mulungu” imene inachitikira mumzindawu, ndipo anthu 278 atsopano anabatizidwa. Taganizirani banja lina lachimwenye limene linafika pamsonkhanowu. Zaka khumi zapitazo, bambo wa m’banjali dzina lake Alan, anauzidwa choonadi cha m’Baibulo ndi mwana wake wamkazi Somashini. Alan anali atangosiya kumwa mowa mwauchidakwa ndipo anali kufunafuna kudziŵa cholinga cha moyo. Somashini, amene panthaŵiyi n’kuti ali ndi zaka zitatu zokha, anawabweretsera bambo ake buku limene analipeza m’nyumba yoyandikana ndi yawo. Mutu wa bukuli wakuti, Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?, nthaŵi yomweyo unam’kopa Alan. Iye anasangalala nazo zimene anaŵerengazo ndipo anayamba kusonkhana ndi Mboni za Yehova. Malingana ndi zimene anaphunzira m’Baibulo, Alan analembetsa mtchatho wa ukwati wake. Posapita nthaŵi mkazi wake Rani anachita chidwi ndipo nayenso anayamba kufika kumisonkhano ya Mboni za Yehova. Panthaŵiyo banjali linali kukhala ndi makolo a Rani, amene ali m’tchalitchi china chachikristu. Makolowo anakana kuti banjali liyambe chipembedzo chawo chatsopano ndipo anawauza kuti musankhepo pa zinthu ziŵiri izi: “Musiyane ndi Amboni apo ayi muchoke m’nyumba yathu ino!”

Alan ndi Rani anaganiza zochoka panyumbapo, ngakhale kuti kupeza kokhala kunali kovuta. Anzawo a m’gulu la Mboni za Yehova anawathandiza kupeza malo okhala abwino ndithu. M’chaka cha 1992, Alan ndi Rani anabatizidwa n’kukhala Mboni za Yehova. Iwo analimbikirabe ndipo pakali pano Alan ndi mkulu mumpingo wachikristu.

M’kati mwa mzinda wa Durban muli mipingo ya Mboni za Yehova yoposa 50. Ndipo yambiri ili ndi Azulu okhaokha. Komabe, mipingo ina, makamaka imene ili pafupi ndi likulu la mzindawu, ili ndi Azulu, Amwenye, ndiponso Azungu. Ngati mutapita ku msonkhano wina wa kumeneku, mukaona kuti si kuti kuli chabe anthu a chikhalidwe chosiyanasiyana. N’kutheka kuti mukapeza munthu wina wakuda wotchena bwino akuyang’anira zinthu, mwinanso Mboni ina yachimwenye kapena yachizungu. Koma chinthu chimodzi chosakayikitsa n’chakuti: Mukakayang’ana pagulu lonselo la anthu, mukadzionera nokha umboni wakuti Baibulo lili ndi mphamvu zogwirizanitsa anthu amitundu yonse kuti akhale mabwenzi okondana ndiponso okhalitsa.

[Chithunzi patsamba 26]

Alan, Rani, ndiponso ana awo

[Chithunzi patsamba 26]

Misonkhano yampingo imabweretsa pamodzi anthu a mafuko onse

[Chithunzi patsamba 26]

Holo ya mumzinda wa Durban

[Mawu a Chithunzi patsamba 25]

Zithunzi: Courtesy Gonsul Pillay