Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyesedwa kwa Chikhulupiriro ku Poland

Kuyesedwa kwa Chikhulupiriro ku Poland

Kuyesedwa kwa Chikhulupiriro ku Poland

YOSIMBIDWA NDI JAN FERENC

NDINALI wachinyamata ndithu pamene Nkhondo Yachiŵiri Yapadziko Lonse inali m’kati. Ndikukumbukira bwinobwino za achimwene awo a bambo anga omwe anali a Mboni za Yehova. Iwo ankabwera kunyumba ndipo ankatiŵerengera Baibulo. Makolo anga analibe nazo chidwi koma mkulu wanga Józef, mlongo wanga Janina, ndi ine tinali n’chidwi kwabasi. Posakhalitsa tonsefe tinasonyeza kudzipatulira kwathu kwa Yehova mwa kubatizidwa. Pamene ndinkabatizidwa n’kuti ndili ndi zaka 14 zokha basi.

Poona mmene phunziro la Baibulo lasinthira bwino kwambiri miyoyo yathu, makolo athu anayamba kumvetsera. Bambo anga atazindikira kuti Baibulo limaletsa kupembedza mafano, iwo anati: “Ngati izi zilidi zimene Mawu a Mulungu amanena, ndiye kuti ansembe ankatibisira. Mwana wanga, tsitsa mafano onse ali pa khoma ndipo ukawataye!” Patangopita zaka pafupifupi ziŵiri, makolo anga anabatizidwa. Iwo anatumikira Yehova mokhulupirika mpaka imfa yawo.

Mavuto Omwe Anatichitikira

Mboni za Yehova zinali pamavuto adzaoneni nkhondo itatha. Mwachitsanzo, ofesi ina ku Lodz pafupi ndi Ofesi ya Zachitetezo inaukiridwa ndipo anthu amene ankagwira ntchito mu ofesiyo anamangidwa. Kum’maŵa kwa dziko la Poland, zigaŵenga zotchedwa National Armed Forces zinalimbikitsidwa ndi atsogoleri achipembedzo chachikatolika n’kuukira a Mboni za Yehova mwankhanza kwambiri. *

Panthaŵiyo n’kuti akuluakulu a boma la Chikomyunizimu atasinthanso maganizo awo pa za chilolezo chomwe anatipatsa kuti titha kuchita misonkhano yathu, ndiponso anayesa kusokoneza misonkhano yomwe inali itayamba kale. Komabe, kutsutsa komakulakulabe kumeneku kunangowonjezera kulimba mtima kwathu kuti tipitirize kulalikira za Ufumu wa Mulungu. Mu 1949 tinali ndi lipoti la Mboni zokwana 14,000 ku Poland.

Pasanapite nthaŵi, ndinakhala mpainiya, mtumiki wanthaŵi zonse wa Mboni za Yehova. Gawo langa loyamba linali pamtunda wokwana makilomita 500 kuchokera kwathu. Komabe, patapita nthaŵi ndinasankhidwa kuti ndikatumikire monga woyang’anira woyendayenda ku dera la kum’maŵa kwa Lublin komwe kunali kufupi ndi kumene makolo anga ankakhala.

Kumangidwa ndi Kuzunzidwa

Mu June 1950, akuluakulu a boma la Chikomyunizimu anandimanga n’kundiimba mlandu wakuti ndinali kazitape wa dziko la United States ndipo anandiika m’selo yachinyontho. Usiku, wapolisi yemwe ankafufuza nkhaniyo ananditulutsa kuti akandifunse mafunso. “Gulu la chipembedzo chanuchi n’lampatuko ndipo ndi mdani wa dziko lathu,” iye anandiuza motero. “Maofesi a likulu lanu amagwira ntchito ya ukazitape wa dziko la America. Umboni tili nawo! Abale ako ena avomera kale kuti anayenda m’dziko lonse lino kuti adziŵe za gulu lathu lankhondo ndiponso za mafakitale opanga zida zankhondo a m’dziko lino.”

Mwachionekere, milandu yonseyi inali yonama. Komabe, wapolisiyo anandilangiza kuti ndisaine chikalata chosonyeza kuti ndachoka m’gulu lomwe iye analitcha kuti “gulu lanu lochititsa manyazi.” Anayesetsa mobwerezabwereza kuti andisainitse chikalatacho. Anafika mpaka pondikakamiza kuti ndilembe maina ndi maadiresi a Mboni zonse zomwe ndimadziŵa komanso malo omwe mabuku athu amachokera. Zofuna zake zonse zinalephereka.

Kenako, apolisi aja anandimenya ndi chibonga mpaka ndinakomoka. Zitatero, anandithira madzi kuti nditsitsimuke, kenako anayambiranso kundifunsa mafunso. Usiku wotsatira ndinamenyedwa kodetsa nkhaŵa m’zidendene. Ndinapempha Mulungu mokweza kuti andipatse mphamvu kuti ndithe kupirira. Ndimadzimva kuti anaterodi. Kundifunsa mafunso usiku koteroko kunkachitika nthaŵi ndi nthaŵi pafupifupi kwa chaka chimodzi.

Ndinatulutsidwa m’ndende mu April 1951, koma a Mboni ena ambiri anali akadali m’ndende. Ndinapita kukapempha ntchito ina kwa wa Mboni yemwe anali ndi udindo. “Kodi sukuchita mantha kuti adzakumanganso?” iye anandifunsa motero. “Panopa ndine wolimba mtima kwambiri kukagwira ntchito kumene kukufunika kwambiri alaliki,” ndinayankha motero. Ndinayambanso ntchito yanga monga woyang’anira woyendayenda ndipo kenako ndinaitanidwa kuti ndizikayendetsa ntchito yosindikiza ndi kugaŵa mabuku athu ku Poland.

Panthaŵiyo, tinkagwiritsa ntchito makina achikale otchedwa mimeograph pochulukitsa magazini a Nsanja ya Olonda. Magazini omwe tinkajambulawo anali osaoneka bwino ndiponso tinkalipira ndalama zambiri pogula mapepala omwenso nthaŵiyo ankapezeka ochepa. Kujambula magazini kumeneko kunkachitikira m’malo obisa monga m’mabalani, m’zipinda zapansi, ndiponso m’zipinda zapamwamba. Kwa anthu amene ankagwidwa, chilango chake chinali kundende basi.

Ndimakumbukira chitsime china chopanda madzi chomwe tinkagwiritsa ntchito. Chinali chozama kwambiri ndipo m’chipupa mwake, pansi ndithu mamita 11 kuchokera pamwamba, munali boo lomwe linkakatulukira ku kachipinda komwe tinkachulukitsiramo magazini. Poloŵa m’chitsimemo, ankachita kutiloŵetsa ndi chingwe. Tsiku lina, akundiloŵetsa m’chitsimemo pogwiritsa ntchito bokosi lalikulu lamatabwa, mosayembekezereka chingwe chinaduka. Ndinagwa pansi pa chitsimecho ndipo mwendo wanga unathyoka. Ndinakakhala m’chipatala kwanthaŵi ndithu, kenako ndinabwereranso kuntchito yojambula magazini pa makina a mimeograph aja.

Panthaŵiyi ndinakumana ndi Danuta, mpainiya wachangu kwambiri. Mu 1956 tinakwatirana ndipo kwa zaka zinayi zotsatira tinatumikira limodzi m’chigawo chapakati cha dziko la Poland. Pomwe chimafika chaka cha 1960 n’kuti tili ndi ana aŵiri ndipo tinaganiza kuti Danuta asiye kaye utumiki wanthaŵi zonse kuti asamalire anawo. Pasanapite nthaŵi yayitali, ine ndinamangidwanso ndipo ulendo uno anandiika m’selo yokhala ndi makoswe ambiri. Patapita miyezi isanu ndi iŵiri, ndinaweruzidwa kuti ndikakhale m’ndende zaka ziŵiri.

Kabwerebwere Kundende

M’ndende yotchedwa Bydgoszcz munali akaidi opitirira 300 ndipo ndinapemphera kwa Yehova kuti ndiziuzako akaidi oona mtima uthenga wa Ufumu. Ndinapempha mkulu wa ndendeyo ngati ndingamagwire ntchito yometa. Ndinadabwa, poona kuti anavomeradi. Posakhalitsa ndinayamba kumeta akaidi ndiponso kuchitira umboni kwa akaidi amene ankaoneka kuti ndi amaganizo abwino.

Mkaidi yemwe ndinkagwira naye ntchito yometa posakhalitsa anamvera zimene ndinkamuuza. Iye mpaka anayamba kuuza ena zinthu zimene anaphunzira m’Baibulo. Posakhalitsa, mkulu wa ndendeyo anatilamula kuti tisiye kulalikira zomwe iye anati ndi “nkhani zokopa anthu kuti aukire.” Mnzanga yemwe ndinkameta nayeyo analimba nazo. Iye analongosola kuti: “Ine kale ndinali kuba, koma tsopano ndinasiya. Kale ndinali chidakwa chosuta fodya, koma tsopano ndinaleka kusuta. Tsopano ndapeza cholinga m’moyo ndipo ndikufuna kukhala wa Mboni za Yehova.”

Atanditulutsa m’ndende, ndinatumizidwa ku Poznan kuti ndikakhale woyang’anira “bekale,” dzina lomwe tinkatchula nyumba yosindikiziramo mabuku. Kumapeto kwa m’ma 1950 mabuku omwe tinkasindikiza anayamba kuoneka mwambambande, chifukwa tinali titaphunzira mmene tingachepetsere kukula kwa masamba amabuku pamakina—kwa ife linali luso lapamwamba zedi—ndiponso kugwiritsa ntchito makina osindikizira mabuku opangidwa ndi a Rotaprint. Mu 1960 tinayamba kusindikiza ndiponso kupanga mabuku.

Pasanapite nthaŵi, munthu wina woyandikana nafe anakatineneza pa zomwe tinkachita ndipo ine ndinamangidwanso. Atanditulutsa mu 1962, ndinapatsidwa ntchito ina ku Szczecin pamodzi ndi anthu ena angapo. Koma tisananyamuke, tinalandira malangizo omwe tinkayesa kuti ndi ochokera kwa abale okhulupirika otiuza kuti mmalo mwake tipite ku Kielce. Komabe, titafika kumeneko tinamangidwa, ndipo ine anandilamula kukakhalanso m’ndende chaka china chimodzi ndi theka. Tinali titaperekedwa ndi anthu onyenga omwe anali m’gulu lathu. Patapita nthaŵi, anthuwo anadziŵika ndipo anawachotsa pa gulu lathu.

M’kupita kwanthaŵi, atanditulutsa m’ndende ndinasankhidwa kukayang’anira ntchito yosindikiza mabuku m’dziko lonse la Poland. Mu 1974, patatha zaka khumi ndikuthaŵathaŵa kuti asandimange, anandithamangitsa mpaka anandigwira n’kundimanga ku Opole. Zitangotero ndinatumizidwa kundende ku Zabrze. “Ntchito yako yaubishopu yatha,” anandiuza motero mkulu wa ndende. “Ngati upitiriza kufalitsa nkhani zako zokopa anthu tikakuika m’chipinda chawekha.”

Kulalikira M’ndende

Komabe ntchito yanga monga mtumiki sinathere pomwepo. Ndi iko komwe, ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi akaidi anzanga aŵiri. M’kupita kwanthaŵi, iwo anapita patsogolo mpaka ndinawabatiza m’bafa lalikulu la m’ndendemo.

Akaidi enanso analabadira uthenga wathu ndipo mu April 1977, tinasonkhana pamodzi kuchita Chikumbutso cha imfa ya Kristu. (Luka 22:19) Kenako patatha miyezi iŵiri, mu June 1977, ananditulutsa ndipo sindinamangidwenso.

Panthaŵiyo n’kuti akuluakulu a boma atayamba kuloleza ntchito yathu. Mosakayikira maulendo odzacheza a mamembala a Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova anathandiza kwambiri. Mu 1977, atatu mwa mamembala ameneŵa analankhula ndi oyang’anira, apainiya, ndiponso Mboni zomwe zakhala kwanthaŵi yaitali za m’mizinda yosiyanasiyana. M’chaka chotsatira, aŵiri a mamembalaŵa analoledwa kuchezerana pa telephoni ndi a ku Ofesi Yoona za Chipembedzo. Komabe, ntchito yathu inali yoletsedwabe mpaka m’chaka cha 1989 pomwe inatsegulidwa. Pakali pano, ku Poland kuli Mboni zachangu pafupifupi 124,000.

Danuta m’zaka zaposachedwazi wakhala asakuyenda nane chifukwa cha kufooka kwa thupi lake, komabe akundilimbikitsa ndiponso akufuna kuti ndipitirize kuyendera mipingo. Ndidzamuyamikira mpaka kalekale chifukwa chondilimbikitsa mwakundithandiza panthaŵi zochuluka zomwe ndinali kumangidwa.

Ndinachitadi bwino zaka 50 zapitazo kusankha kutumikira Yehova Mulungu. Ndakhala ndi chimwemwe chadzaoneni pom’tumikira ndi mtima wonse. Mkazi wanga ndi ine taona zimene mawu opezeka pa Yesaya 40:29 amanena zikuchitikadi. Mawuwa amati: “Iye [Yehova] alimbitsa olefuka, nawonjezera mphamvu iye amene alibe mphamvu.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Onani 1994 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 213-22.

[Zithunzi patsamba 29]

Tinkasindikiza mabuku pogwiritsa ntchito makina a “mimeograph” ndipo kenako tinkagwiritsa ntchito makina opangidwa ndi a Rotaprint

[Zithunzi patsamba 30]

Mkazi wanga Dunuta, ndi ine