Yandikirani kwa Yehova

Mulungu akufuna kuti mukhale bwenzi lake. Bukuli likusonyezani mfundo za m’Baibulo zimene mungatsatire kuti mukwanitse kuchita zimenezi.

Mawu Oyamba

Mukhoza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu.

MUTU 1

“Taonani, Uyu Ndiye Mulungu Wathu”

N’chifukwa chiyani Mose anafunsa dzina la Mulungu pamene ankalidziwa kale?

MUTU 2

Kodi ‘Mungayandikiredi Kwa Mulungu’?

Yehova Mulungu, yemwe analenga kumwamba ndi dziko lapansi akutiitana kuti timuyandikire ndipo watipatsa lonjezo.

MUTU 3

“Woyera, Woyera, Woyera, Yehova”

N’chifukwa chiyani Baibulo limayerekezera chiyero ndi kukongola?

CHIGAWO CHOYAMBA

“Wolimba Mphamvu”

MUTU 4

“Yehova Ndiye . . . wa Mphamvu Yaikulu”

Kodi tiyenera kuopa Mulungu chifukwa choti ndi wamphamvu? Tingati inde komanso ayi.

MUTU 5

Mphamvu za Kulenga—“Amene Analenga Zakumwamba ndi Dziko Lapansi”

Tikaganizira zinthu zazikulu zimene Mulungu analenga monga dzuwa komanso zinthu zing’onozing’ono monga timbalame, tingaphunzire zambiri zokhudza iye.

MUTU 6

Mphamvu Zowononga—‘Yehova Ndi Munthu Wankhondo’

N’chifukwa chiyani “Mulungu wamtendere” nthawi zina amamenya nkhondo?

MUTU 7

Mphamvu Zoteteza—“Mulungu Ndiye Pothaŵirapo Pathu”

Mulungu amateteza atumiki ake mwa njira ziwiri, koma njira inayo ndiyofunika kwambiri.

MUTU 8

Mphamvu Zobwezeretsa—Yehova ‘Akupanga Zonse Kukhala Zatsopano’

Panopa Yehova wabwezeretsa kale kulambira koona. Kodi m’tsogolomu adzabwezeretsa chiyani?

MUTU 9

“Kristu Mphamvu ya Mulungu”

Kodi zozizwitsa komanso zinthu zimene Yesu ankaphunzitsa zimasonyeza chiyani zokhudza Mulungu?

MUTU 10

‘Khalani Otsanzira Mulungu’ Pamene Mukugwiritsa Ntchito Mphamvu

Mutakhala ndi mphamvu zambiri, kodi mungatati kuti muzizigwiritsa ntchito moyenera?

MUTU 11

Njira Zake Zonse Ndi Chilungamo

N’chifukwa chiyani khalidwe la Mulungu la chilungamo lili lochititsa chidwi kwambiri?

MUTU 12

“Kodi Chilipo Chosalungama ndi Mulungu?”

Ngati Mulungu amadana ndi zopanda chilungamo, n’chifukwa chiyani padzikoli pali zinthu zopanda chilungamo zambiri?

MUTU 13

“Malamulo a Yehova Ali Angwiro”

Kodi malamulo angalimbikitse bwanji chikondi?

MUTU 14

Yehova Alinganiza “Dipo la Anthu Ambiri”

Chiphunzitso chosavuta kumva koma chofunika chingakuthandizeni kuyandikira Mulungu.

MUTU 15

Yesu Akhazikitsa Chilungamo M’dziko Lapansi

Kodi Yesu analimbikitsa bwanji chilungamo m’mbuyomu? Kodi akuchirimbikitsa bwanji masiku ano? Ndipo adzachita bwanji zimenezi m’tsogolo?

MUTU 16

‘Chitani Cholungama’ Poyenda ndi Mulungu

N’chifukwa chiyani Yesu anachenjeza kuti: “Musaweruze, kuti mungaweruzidwe.”?

CHIGAWO CHACHITATU

“Wa Mtima Wanzeru”

MUTU 17

‘Ha! Kuya Kwake kwa Nzeru za Mulungu!’

N’chifukwa chiyani nzeru za Mulungu zimaposa, kudziwa kwake zinthu, kumvetsa komanso kuzindikira?

MUTU 18

Nzeru mu “Mawu a Mulungu”

N’chifukwa chiyani Mulungu anagwiritsa ntchito anthu kulemba Baibulo mmalo mogwiritsa ntchito angelo kapena kulemba yekha?

GAWO 19

“Nzeru ya Mulungu M’chinsinsi Chopatulika”

Kodi pangano latsopano lomwe kale Mulungu analibisa ndipo tsopano analiulula ndi lotani?

MUTU 20

“Wa Mtima Wanzeru”—Komatu Wodzichepetsa

Kodi n’zotheka bwanji kuti Mlengi wachilengedwe chonse akhale wodzipetsa?

MUTU 21

Yesu Anaulula “Nzeru ya kwa Mulungu”

Kodi Yesu ankaphunzitsa bwanji kuti asilikali omwe anatumidwa kukamugwira abwereko chimanjamanja?

MUTU 22

Kodi ‘nzeru ya Kumwamba’ Ikugwira Ntchito mwa Inu?

Baibulo limafotokoza njira 4 zimene zingakuthandizeni kupeza nzeru ya Mulungu kapena kuti nzeru ‘yochokera kumwamba.’

MUTU 23

“Anayamba iye Kutikonda”

Kodi mawu akuti ‘Mulungu ndi chikondi’ amatanthauza chiyani kwenikweni?

MUTU 24

Palibe ‘Chingatisiyanitse ndi Chikondi cha Mulungu’

Tsutsani bodza lakuti Mulungu sakukondani ndiponso kuti ndinu osafunika kwa iye.

MUTU 25

“Mtima Wachifundo wa Mulungu Wathu”

Kodi Yehova amamva bwanji akamakuonani inuyo mofanana ndi mmene mayi amachitira ndi mwana wake?

MUTU 26

Mulungu “Wokhululukira”

Ngati Mulungu amakumbukira chilichonse ndiye zimatheka bwanji kuti azikhululuka ndiponso kuiwalako zimene tinalakwitsa?

MUTU 27

“Ubwino Wake ndi Waukulu Ndithu”

Kodi ubwino wa Mulungu umatanthauza chiyani kwenikweni?

GAWO 28

“Inu Nokha Ndinu Wokhulupirika”

N’chifukwa chiyani khalidwe lomwe Mulungu ali nalo la kukhulupirika limaposa khalidwe lake la kukhala wodalirika?

MUTU 29

“Kuzindikira Chikondi cha Kristu”

Mbali zitatu za chikondi cha Khristu zimasonyeza bwino chikondo cha Yehova.

MUTU 30

“Yendani M’chikondi”

Lemba la 1 Akorinto 14 limasonyeza njira zimene tingasonyezere chikondichi.

MUTU 31

“Yandikirani kwa Mulungu, Ndipo Adzayandikira kwa Inu”

Kodi muyenera kudzifunsa funso lofunika liti? Nanga mungayankhe bwanji?