‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’

Cholinga cha bukuli si kufotokoza mwachidule nkhani yonse ya moyo ndi utumiki wa Yesu, koma kutithandiza kudziwa bwino zimene tingachite kuti tizimutsatira.

Mawu Oyamba

Muzikonda kwambiri Yesu komanso muzimutsatira mosamala kwambiri kuti muzisangalatsa mtima wa Yehova panopa mpaka m’tsogolo.

MUTU 1

Kodi Yesu Ankatanthauza Chiyani Pamene Ananena Kuti ‘Ukhale Wotsatira Wanga’?

Kukhala wotsatira weniweni wa Yesu kumafuna zambiri, osati zolankhula zathu zokha kapena zimene tikuganiza.

MUTU 2

“Njira Choonadi ndi Moyo”

Tingafike kwa Mulungu kudzera mwa Yesu basi. Atate wamupatsa udindo wofunika kwambiri pokwaniritsa zolinga zake zonse.

MUTU 3

“Ndine . . . Wodzichepetsa”

Yesu anali wodzichepetsa pa nthawi yonse imene ankachita utumiki wake padziko lapansi.

MUTU 4

“Taona! Mkango wa Fuko la Yuda”

Yesu anasonyeza kulimba mtima ngati mkango pamene anachita zinthu zitatu izi: kuteteza choonadi, kutsatira chilungamo ndiponso pamene ankatsutsidwa.

MUTU 5

“Chuma Chonse Chokhudzana ndi Nzeru”

Mawu komanso zochita za Yesu zinasonyeza kuti anali ndi nzeru zakuya.

MUTU 6

“Anaphunzira Kumvera”

Popeza Yesu anali kale wangwiro ndipo ankamvera Atate ake n’chifukwa chiyani tikunena kuti “anaphunzira kumvera” komanso kuti ‘anakhala wangwiro’ atabwera padzikoli?

MUTU 7

“Ganizirani Mozama za Munthu Amene Anapirira”

Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri cha kupirira. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kupirira? Kodi tingati kuti tikhale opirira ngati Yesu?

MUTU 8

“Ndi Zimene Mulungu Anandituma Kudzachita”

Onani chifukwa chimene Yesu ankalalikirira, uthenga umene ankalalikira ndiponso mmene ankaonera ntchito yake yolalikirayi pamene anali padziko lapansi.

MUTU 9

“Pitani Mukaphunzitse Anthu . . . Kuti Akhale Ophunzira Anga”

Otsatira enieni a Khristu amadziwika chifukwa chogwira ntchito yophunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu.

MUTU 10

“Malemba Amati”

Tingatsanzire zimene Yesu ankachita pouza ena choonadi ngati timatchula mfundo za m’Mawu a Mulungu, timateteza Baibulo komanso ngati timafotokoza tanthauzo la mawuwo.

MUTU 11

“Palibe Munthu Amene Analankhulapo Ngati Iyeyu N’kale Lonse”

Tiyeni tikambirane njira zitatu zimene Yesu ankagwiritsa ntchito pophunzitsa ndipo tione mmene ifeyo tingamutsanzirire.

MUTU 12

“Nthawi Zonse Iye Ankalankhula Nawo Pogwiritsa Ntchito Mafanizo”

Baibulo limanena zifukwa ziwiri zofunika kwambiri zimene zinachititsa kuti Yesu azigwiritsa ntchito mafanizo.

MUTU 13

“Ndimakonda Atate”

Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pa nkhani yokonda kwambiri Yehova?

MUTU 14

“Anthu Ochuluka Anabwera kwa Iye”

Anthu ambiri kuphatikizapo ana ankamasuka kupita kwa Yesu. N’chifukwa chiyani anthu ankapita kwa Yesu momasuka?

MUTU 15

“Anagwidwa ndi Chifundo”

N’chifukwa chiyani n’zofunika kwambiri kuti tizitsanzira Yesu pa nkhani yochitira ena chifundo

MUTU 16

“Yesu . . . Anawakonda Mpaka pa Mapeto a Moyo Wake”

Pa utumiki wake wonse, anasonyeza m’njira zambiri kuti ankakonda atumwi akewo. Kodi tingasonyeze bwanji chikondi chimenechi tikamachita zinthu ndi ena?

MUTU 17

“Palibe Amene Ali ndi Chikondi Chachikulu Kuposa Ichi”

Kodi tingatsanzire Yesu m’njira ziti posonyeza chikondi chodzimana?

MUTU 18

“Pitiriza Kunditsatira”

Tikapitiriza kutsatira Yesu tsiku ndi tsiku, tidzakhala ndi chikumbumtima choyera komanso tidzayembekezera zinthu zabwino m’tsogolo.