Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Mmene Mungayambire Kucheza ndi Anthu Kuti Muwalalikire Mwamwayi

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Mmene Mungayambire Kucheza ndi Anthu Kuti Muwalalikire Mwamwayi

Yesu analalikira mwamwayi mayi wachisamariya chifukwa choti anayamba ndi kucheza naye. Kodi tingatani kuti tisamavutike kuyamba kucheza ndi anthu n’cholinga choti tiwalalikire?

  • Muzikhala ochezeka mukamayankhula ndi anthu. Ngakhale kuti anali atatopa, Yesu anayamba kuyankhula ndi mayi uja pomupempha madzi akumwa. Mungathe kuyamba kucheza ndi munthu pomupatsa moni mwansangala ndipo kenako mungatchule nkhani zokhudza mmene nyengo ilili kapena nkhani zina zimene zangochitika kumene. Muzikumbukira kuti cholinga chanu ndi kungoyamba kucheza ndi munthuyo choncho mukhoza kuyambitsa nkhani iliyonse imene ingamuchititse chidwi. Ngati sanakuyankheni, musadandaule. Mungayesenso kucheza ndi munthu wina. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala wolimba mtima.​—Neh. 2:4; Mac. 4:29.

  • Muzikhala tcheru kuti mupeze mpata wolalikira uthenga wabwino, koma musamachite zinthu mopupuluma. Mungacheze ndi munthuyo kwa kanthawi mpaka mutaona kuti mukhoza kumulalikira. Mukachita zinthu mopupuluma, munthuyo angaipidwe n’kusiya kukumvetserani. Musakhumudwe ngati mwasiya kukambirana musanamulalikire. Ngati zimakuvutani kuyamba kulalikira mwamwayi, mungachite bwino kungokhala ndi cholinga choti muzicheza nawo popanda kuwalalikira mpaka mutazolowera. [Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyo yoyamba.]

  • Mukamacheza, muziyesa kunena zinazake zimene zingakuthandizeni kuti mulalikire. Mwachitsanzo, munganene zimene mumakhulupirira m’njira yoti munthuyo akufunseni funso. Yesu ananena zinthu zimene zinachititsa mayi uja kuti amufunse mafunso. Pamene ankayankha mafunsowo, anapeza mwayi womuuza uthenga wabwino. [Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyo yachiwiri, kenako oneraninso ndi kukambirana mfundo za m’vidiyo yachitatu.]