Uthenga Wabwino wa Yesu

Mumavidiyowa muphunzira zambiri zokhudza Yesu Khristu mwana wa Mulungu komanso Mpulumutsi.

Zimene Zili M’mavidiyo Akuti; Uthenga Wabwino wa Yesu

Onerani nkhani za m’mabuku a Uthenga Wabwino zomwe zikuoneka ngati zikuchitikadi m’mavidiyo osangalatsa amenewa okhudza Yesu Khristu

GAWO 1

Kuwala Kwenikweni kwa Dziko

Yosefe ndi Mariya akupatsidwa mwayi wamtengo wapatali wolera Yesu, yemwe anali wosiyana ndi ana ena onse.

GAWO 2

“Uyu Ndi Mwana Wanga”

Yohane M’batizi akulengeza za kuonekera kwa Mesiya. Yesu akuyamba utumiki wake.

GAWO 3

“Munthu Ameneyo Ndi Ineyo”

Yesu akuphunzitsa Nikodemo, mayi wa ku Samariya, komanso anthu a ku Nazareti koma anthuwo akulandira uthenga wake mosiyanasiyana.

GAWO 4

“Chifukwa Ndinabwera Kudzachita Zimenezi”

Yesu akuchiritsa odwala, akutulutsa ziwanda, akuphunzitsa anthu komanso akusankha atumwi ake 12.

GAWO 5

“Anadabwa Kwambiri ndi Kaphunzitsidwe Kake”

Pambuyo pochiritsa gulu la anthu, Yesu akuyamba ulaliki wapaphiri womwe ndi wotchuka kwambiri.

GAWO 6

“Kodi Mesiya Amene Tikumuyembekezera uja Ndi Inu?”

Yesu akuukitsa mwana wa mayi wamasiye, akuphunzitsa pogwiritsa ntchito mafanizo osavuta kumva, ndipo akusonyeza poyera zolinga za anthu amene akumumvetsera.