MALO A NKHANI

Ukraine

Chichewa
Ukraine
/assets/ct/28ada02fb0/images/syn_placeholder_sqr.png

Ukraine

 

2019-08-12

UKRAINE

A Mboni za Yehova ku Ukraine Anaonetsa Anthu Mabaibulo M’malo Osiyanasiyana

A Mboni za Yehova ku Ukraine anachita zionetsero zapadera za Baibulo pofuna kudziwitsa anthu za kutulutsidwa kwa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la Chinenero Chamanja cha ku Russia.

2018-11-26

UKRAINE

A Mboni za Yehova Anasonyeza Mtima Wochereza Komanso Mgwirizano pa Msonkhano Wapadera ku Ukraine

A Mboni za Yehova mumzinda wa Lviv ku Ukraine, analandira abale ndi alongo awo masauzande ambiri ochokera kumayiko ena omwe anakachita nawo msonkhano wapadera wachigawo. Alendo anasangalala ndi kuona malo komanso zinthu zachikhalidwe.

2018-11-02

UKRAINE

Chipembedzo cha Mboni za Yehova Chaletsedwa ku “Donetsk People’s Republic”

Khoti Lalikulu Kwambiri ku DPR laletsa chipembedzo cha Mboni za Yehova ndipo imeneyi ndi njira yowazunzira imene khotili lagwiritsa ntchito posachedwapa kum’mawa kwa Ukraine.

2017-07-31

UKRAINE

Akuluakulu a Boma ku Ukraine Anakaona Malo ku Ofesi ya Mboni za Yehova Patsiku Lapadera

Kwa nthawi yoyamba kuchokera mu 2001, ofesi ya mboni za Yehova ku Ukraine inakonza tsiku lapadera kuti anthu adzaone ntchito zimene zimachitika paofesiyo ndipo zimene zinachitika pa 2 May, 2017.

2018-01-17

UKRAINE

Khoti Lalikulu ku Ukraine Linalimbikitsa Ufulu Wosonkhana Mwamtendere

Panopo a Mboni za Yehova ku Ukraine akhoza kupanga lendi malo kuti achitiremo mapemphero popanda kukanizidwa.

2019-03-26

UKRAINE

Khoti Lalikulu ku Ukrain Lagamula Kuti Anthu Ali ndi Ufulu Wokana Kulowa Usilikali pa Zifukwa za Chipembedzo

Khoti lalikulu lagwirizana ndi zimene makhoti ang’onoang’ono anagamula zoti munthu ali ndi ufulu wokana kulowa usilikali ngakhale pa nthawi yomwe m’dziko muli ziwawa za ndale kapena nkhondo.

2016-01-26

UKRAINE

A Mboni Anaulutsa Msonkhano Wapadera Kudera Limene Kunali Nkhondo ku Ukraine

A Mboni za Yehova a ku Ukraine anakhala ndi msonkhano wapadera pa 14 February 2015 kuti alimbikitse Akhristu anzawo oposa 17,000 omwe ali m’dera limene kunali nkhondo.

2016-03-02

UKRAINE

Makhoti a ku Ukraine Avomereza Kuti Munthu Ali ndi Ufulu Wokana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Makhoti a ku Ukraine anagamula kuti boma silingachotse ufulu wa munthu wotsatira zimene amakhulupirira chifukwa chofuna kuteteza dziko.

2015-03-10

UKRAINE

A Mboni za Yehova Akuthandiza Anthu Ambiri Amene Akusowa Pokhala ku Ukraine

Ofesi ya Mboni za Yehova ya ku Ukraine ikupitiriza kuthandiza a Mboni ambiri amene akusowa pokhala chifukwa cha nkhondo kum’mawa kwa dziko la Ukraine.

2014-12-03

UKRAINE

A Mboni za Yehova Anachita Msonkhano Mwamtendere ku Ukraine Ngakhale Kuti Kuli Nkhondo

Ngakhale kuti nkhondo yavuta kum’mawa kwa dziko la Ukraine, anthu ambiri anasonkhana ku Lviv kuti achite msonkhano wakuti “Pitirizani Kufunafuna Ufumu wa Mulungu Choyamba.” Pamsonkhanowu anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lokonzedwanso lomwe linamasuliridwa m’Chiyukireniya.

2014-08-19

UKRAINE

Anthu Akuvulazidwabe ku Ukraine Chifukwa Chakuti Olakwa Sakupatsidwa Chilango

Anthu omwe akuvutitsa anzawo chifukwa chodana ndi chipembedzo chawo sakupatsidwa chilango chilichonse. A Mboni za Yehova omwe ndi anthu okonda mtendere akupitirizabe kuvutitsidwa.

2014-08-19

UKRAINE

Lipoti Lokhudza Mboni za Yehova ku Ukraine ndi ku Crimea

A Mboni za Yehova adzachita misonkhano yoposa 40 ku Ukraine ndi ku Crimea ngakhale kuti m’mayikowa zinthu sizikuyenda bwino. Misonkhanoyi idzafotokoza za mmene anthu tizidzakhalira mwantendere Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira.