Philippines
A Mboni za Yehova Akugwira Ntchito Yokonza Zinthu Zomwe Zinaonongeka ndi Mvula Yamkuntho Yotchedwa Nock-Ten
A Mboni za Yehova akugwira nawo ntchito yokonzanso ndi kumanga nyumba zambirimbiri zomwe zinaonongedwa kapena kugwa ndi mvula yamkuntho ku Philippines chakumapeto kwa 2016.
Anthu Amene Anakhudziwa ndi Mphepo Yamkuntho Yotchedwa Typhoon Haiyan Tsopano Amangiridwa Nyumba
Mphepo yamkuntho yotchedwa Typhoon Haiyan itawononga zinthu, a Mboni za Yehova anagwira ntchito yaikulu yomanga nyumba pafupifupi 750.
Nkhani Mwachidule: A Mboni za Yehova Akonza Ntchito Yothandiza Anthu Amene Anakhudzidwa ndi Mvula Yamkuntho ya Haiyan
Ntchito yothandiza anthu amene anakhudzidwa ndi ngozi ikuchitika ku Philippines ndipo amene akugwira ntchitoyi ndi anthu ongodzipereka. Katundu wokwana matani 190 wothandizira anthu wakhala akutumizidwa ku Phillipines.
Mvula Yoopsa Yamkuntho, Yotchedwa Haiyan Yasakaza Zinthu Kwambiri M’dera Lapakati ku Philippines
Mvula yoopsa yamkuntho, yotchedwa Haiyan inapha anthu komanso kuwononga zinthu ku Philippine. A Mboni za Yehova akugwira ntchito yothandiza anthu okhudzidwa ndi tsokali mogwirizana ndi akuluakulu a boma.

