KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kuphunzitsa Anthu Pogwiritsa Ntchito Kabuku ka Uthenga Wabwino
-
Werengani funso limene lalembedwa m’zilembo zakuda kwambiri kuti mwininyumba aganizire kwambiri mfundo yaikulu.
-
Werengani ndime yake.
-
Werengani malemba akuda kwambiri ndipo funsani mafunso amene angathandize munthuyo kuti apeze yankho la funso lija pa ndimeyo.
-
Ngati m’munsi mwa funsolo muli ndime inanso, bwerezani mfundo 2 ndi 3. Ngati pa jw.org/ny pali vidiyo yomwe ikugwirizana mafunsowo, muonetseni mwininyumbayo.
-
Kuti mutsimikizire ngati mwininyumbayo wamvetsa mfundo yaikulu, mufunseni mafunso akuda kwambiri aja.