Zokhudza Inu
Kodi ndinu ndani? Nanga mumayendela mfundo ziti pa umoyo? Ngati mungadzidziwe bwino, mudzatha kusankha nokha zocita pa moyo wanu m’malo moti anthu ena azikusankhilani.
Khalidwe Langa
Kodi Nifuna Kukhala Munthu Wabwanji?
Kudziŵa makhalidwe ako abwino, zimene umacita bwino, zimene sucita bwino, na zolinga zako, kudzakuthandiza kupanga zosankha zanzelu ukakumana na ciyeso.
N’cifukwa Ciyani Muyenela Kukhala Woona Mtima?
Kodi muyenela kunama kuti mupambane? Dzioneleni nokha cifuwa cake kukhala woona mtima ndi kwaphindu.
Musagonje Anzanu Pokunyengelelani!
Zinthu 4 zimene zingakuthandizeni kuti muzisankha nokha zocita mwanzelu.
Zocita Zanga
Zifukwa Zokhalila ndi Cikhulupililo—Mmene Tiyenela Kucitila Zinthu ndi Ena
Kodi zimene anthu ena amanena zingakhudze bwanji mmene timacitila zinthu ndi anthu ena? Paola ndi Mikel afotokoza mmene Baibo inawathandizila.
Maonekedwe Anga
Zimene Acinyamata Amakamba Zokhuza Maonekedwe
N’cifukwa ciyani zimakhala zovuta kwa acinyamata kukhala na maganizo oyenela pa maonekedwe awo? N’ciyani cingaŵathandize?
Nimadelanji Nkhawa na Mmene Nimaonekela?
Kodi sumakondwela na mmene umadzionela pa gilasi? Nanga ungacite ciani kuti uzioneka bwino?

