Cinyanja
NSANJA YA MLONDA Amuna Anayi Okwela pa Mahosi—Kodi Amakukhudzani Bwanji?
https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/wp/201705/CIN/pt/wp_CIN_201705_lg.jpg

NSANJA YA MLONDA Na. 3 2017 | Amuna Anayi Okwela pa Mahosi—Kodi Amakukhudzani Bwanji?

MUGANIZA BWANJI?

Nkhani ya amuna anayi okwela pa mahosi ni imodzi mwa nkhani zodziŵika kwambili m’buku la Chivumbulutso. Anthu ena amacita nayo mantha. Ena amacita nayo cidwi. Onani zimene Baibo imakamba zokhudza maulosi monga amenewa:

“Wodala ndi munthu amene amaŵelengela ena mokweza, ndiponso anthu amene akumva mau a ulosi umenewu.”Chivumbulutso 1:3.

Magazini iyi ya Nsanja ya Mlonda, ifotokoza mmene tingapindulile na nkhani ya amuna anayi okwela pa mahosi.

 

NKHANI YA PACIKUTO

Mmene Amuna Anayi Okwela pa Mahosi Amakukhudzilani

Mahosi anayi—yoyela, yofiila, yakuda, ndi yotuŵa. Nkhani ya amuna anayi okwela pa mahosi ni yodziŵika kwambili m’buku ya Chivumbulutso.

NKHANI YA PACIKUTO

Kodi Amuna Anayi Okwela pa Mahosi N’ndani?

Ŵelengani kuti mudziŵe tanthauzo la masomphenya amenewa.

Umboni Winanso

Mwina simungadziŵe kuti Tatenai anali ndani, koma umboni wa zinthu zakale utsimikizila za munthu ameneyu.

BAIBO IMASINTHA ANTHU

N’nali Kukonda Baseball Kuposa Cina Ciliconse

Samuel Hamilton anali woloŵelela kwambili m’zamasewela, koma kuphunzila Baibo kunasintha umoyo wake.

TENGELANI CIKHULUPILILO CAWO

“Ndiwe Mkazi Wokongola M’maonekedwe Ako”

Ali mu Iguputo, akalonga a Farao anaona kuti Sara anali wokongola kwambili. Zimene zanacitika zingakudabwitseni.

Kodi Baibo Imakamba Ciani?

Kodi Mulungu amakondela? Kodi anthu ena ni odalitsidwa, pamene ena ni otembeleledwa?