Magazini a Nsanja ya Mlonda ndi Galamuka!
Magazini athu amenewa ali ndi nkhani zozikidwa pa Baibo ndipo akupezeka mu zinenelo mahandiledi, kuphatikizapo zinenelo za manja. Nsanja ya Mlonda imafotokoza za uthenga wabwino wokamba za Ufumu wa Mulungu, ndiponso imalimbikitsa cikhulupililo mwa Yesu Khristu. Galamuka! imatithandiza mmene tingalimbanilane ndi mabvuto a masiku ano. Imatithandizanso kukhulupilila malonjezo a Mlengi wathu a dziko latsopano la bata ndi mtendele.

