Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

GALAMUKA! Na. 1 2022 | Mungadziteteze Bwanji ku Mavuto a m’Dzikoli?

Pamene mavuto akuculukila-culukila m’dzikoli, ambili a ife tikuvutika cifukwa ca matsoka a zacilengedwe komanso mavuto ena ocititsidwa na anthu. Phunzilani mmene mungadzitetezele ku mavuto amenewa, komanso mmene mungatetezele anthu amene mumakonda.

 

Kodi Mungadziteteze Bwanji ku Mavuto a m’Dzikoli?

Mukakumana na mavuto aakulu, yesetsani kudziteteza pamodzi na a m’banja lanu.

1 | Tetezani Thanzi Lanu

Mukamateteza thanzi lanu, mpamenenso mudzakwanitsa kupilila mavuto othetsa nzelu.

2 | Tetezani Cuma Canu

Ngati mumaseŵenzetsa bwino ndalama zanu, mudzakwanitsa kupilila pa nthawi ya mavuto.

3 | Tetezani Ubale Wanu na Ena

Onani mfundo zimene zingakuthandizeni kuteteza ukwati wanu, ubwenzi wanu na ana anu komanso na anthu ena.

4 | Limbitsani Ciyembekezo Canu

Baibo imatithandiza kupilila mavuto komanso imatipatsa ciyembekezo ca tsogolo labwino.

M’kope Ino ya Galamuka!

Ŵelengani nkhani izi kuti mudziŵe mmene mungadzitetezela pamodzi na banja lanu ku mavuto amene tikukumana nawo m’dzikoli.