Mbili ya Umoyo wa Yesu
Dziŵani zambili zokhudza Yesu Khristu, amene ni Mwana wa Mulungu komanso Mpulumutsi wa anthu, mu vidiyo yokondweletsa iyi ya mbali zingapo.
Mbili ya Umoyo wa Yesu—Cidule ca Mavidiyo
Onani zocitika zopezeka m’Mabuku a Uthenga Wabwino m’mavidiyo osangalatsa ofotokoza za Yesu Khristu.
Gao 1: Kuwala Kwenikweni kwa Dziko
Kodi anthu adzapulumutsidwa motani ku ucimo umene unayambitsidwa na Adamu? Ni Mesiya yekha amene adzapulumutsa mtundu wa anthu.
Gao 2: “Uyu Ndiye Mwana Wanga”
Yohane M’batizi anakonza njila ya Mesiya. Onani zinthu zocititsa cidwi zimene zinacitika kuciyambi kwa utumiki wa Yesu wa padziko lapansi!
Gao 3: “Ndine Amene”
Yesu akudzidziwikitsa kwa Nikodemo, mai wa Cisamariya, komanso kwa anthu a ku Nazareti kuti ndiyedi Mesiya, koma ndi anthu ocepa cabe amene kumukhulupilila. Pambuyo pocita cozizwitsa, iye akuitana asodzi kuti akhale ophunzila ake.
Gao 4: “Cifukwa n’Cimene n’Nabwelela”
Yesu anaonetsa mphamvu zake mwa kucilitsa odwala komanso kutulutsa ziwanda. Koma ena anatsutsa zimene iye anali kucita ndipo anafuna kumupha. Cifukwa cakuti Yesu anaonetsa cifundo cacikulu ndi kuphunzitsa mwaluso kwambili, iye anapanga ophunzila komanso kusankha atumwi 12.
Gao 5: “Anadabwa Kwambili ndi Kaphunzitsidwe Kake”
Pambuyo pocilitsa khamu la anthu, Yesu anayamba kuphunzitsa anthuwo mnjila imene palibe mphunzitsi aliyense amene anaigwilitsilapo nchito. Khamu la anthu linadabwa kwambili ndi mphamvu zimene Yesu anali nazo, komanso luso logwilitsila nchito mafanizo pophunzitsa.
Gao 6: “Kodi Mesiya Uja Amene Tikuyembekezela Ndinu?”
Yesu aonetsa kuti ali ndi mphamvu zoukitsa akufa. Zozizwitsa zimene akucita komanso ziphunzitso zake, ziulula zolinga zimene omumvetsela ali nazo. Yesu afotokoza za Ufumu mwa kugwilitsila nchito mafanizo.
Mbili ya Umoyo wa Yesu—Dyonkho ya Mavidiyo Ofotokoza Mbili ya Umoyo wa Yesu
Tambani dyonkho ya mavidiyo otsatizana oonetsa bwino zocitika za m’Mabuku a Uthenga Wabwino.

