Pulogilamu ya Msonkhano Wacigao wa Mboni za Yehova wa 2026
Tsiku Loyamba
Pulogilamu ya tsiku loyamba lacokela pa Mateyo 5:3—“Acimwemwe ndi anthu ozindikila zosowa zao zauzimu.”
Tsiku Laciwili
Pulogilamu ya tsiku laciwili lacokela pa Macitidwe 20:35—“Kupatsa kumabweletsa cimwemwe cacikulu kuposa kulandila.”
Tsiku Lothela
Pulogilamu ya tsiku lothela lacokela pa Mateyo 13:16—“Koma inu ndinu acimwemwe cifukwa maso anu amaona, ndipo matu anu amamva.”
Mau Kwa Osonkhana
Malangizo Othandiza kwa Opezeka pa Msonkhano.
Mungakondenso Izi
ZOKHUDZA IFE
Mukapezekepo pa Msonkhano wa 2026 wakuti: “Cimwemwe Camuyaya”
Tikukupemphani kuti mukapezekepo pamsonkhano wacigao wa masiku atatu wa caka cino wa Mboni za Yehova.
MISONKHANO IKULUIKULU
Tikukuitanani ku: Msonkhano Wacigao wa Mboni za Yehova wa 2026 Wakuti “Cimwemwe Camuyaya”
Mudzabwele ku Msonkhano Wacigao wa 2026 wakuti “Cimwemwe Camuyaya” kuti mukamve mmene kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mlengi wathu kungatithandizile kukhala ndi cimwemwe camuyaya.
MISONKHANO IKULUIKULU
Kadyonkho ka Sewelo Lalikulu la m’Baibo: Mbili ya Umoyo wa Yesu: Zigao 4, 5, ndi 6
N’cifukwa ciani anthu anali kukopeka naye Yesu, nanga n’ciani cinacitika pamene zokamba zake zinatsutsa ziphunzitso zacikhalile za Ciyuda?

