Cinyanja
Mbili ya Umoyo wa Yesu
https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/1011760/univ/art/1011760_univ_sqr_xl.jpg

Mbili ya Umoyo wa Yesu—Cidule ca Mavidiyo

MAVIDIYO OTSATIZANA


Dyonkho

Cizindikilo ca cinenelo.

Apezeka m’Zinenelo Zoposa 500

Mavidiyowa akuthandiza anthu padziko lonse, kudziwa zimene Yesu anaphunzitsa, mwa kuonelela mavidiyowa m’zinenelo zao

Cizindikilo ca Baibo.

Mau a m’Mavidiyowa Atengedwa M’Baibo

Mau a m’Mavidiyo amenewa atengedwa m’Mabuku a Uthenga Wabwino a Mateyo, Maliko, Luka, ndi Yohane

Cizindikilo cofufuzila.

Anafufuza Mokwanila

Tinafufuza kwa zaka zambili zocitika za m’mavidiyowa, kuti zikhale zolondola kwambili


Magao Ake

Magao a mavidiyo amenewa ali ndi mau ofotokozela zimene zikuonetsedwa, pothandiza anthu akhungu ndi amene sayang’ana bwino kumvetsa zimene zikuonetsedwa.

GAO 1

Yosefe ndi Mariya apatsidwa mwayi wolela Yesu, mwana wapadela.

GAO 2

Yohane M’batizi alengeza za kuonekela kwa Mesiya. Yesu ayamba utumiki wake.

GAO 3

Yesu aphunzitsa Nikodemo, mai wacisamariya, ndi anthu a ku Nazareti, ndipo akumulandila mosiyanasiyana.

GAO 4

Yesu acilitsa odwala, kutulutsa ziwanda, kupanga ophunzila, ndi kusankha atumwi ake 12.

GAO 5

Pambuyo pocilitsa khamu la anthu, Yesu ayamba Ulaliki wa pa Phili, umene ndi ulaliki wake wochuka kwambili.

GAO 6

Yesu aukitsa mwana wa mkazi wamasiye, aphunzitsa mwa kugwilitsila nchito mafanizo osabvuta, komanso abvumbula zolinga za amene akumumvetsela.

Magao Ena Atuluka Posacedwa

Caka ciliconse, magao atsopano azitulutsidwa mpaka magao onse 18 atatulutsidwa. Magao otsatila adzatulutsidwa mu May 2027.


Kodi Zimene Yesu Anaphunzitsa Zingakuthandizeni Bwanji pa Umoyo Wanu?

Mboni za Yehova ndi zokonzeka kukuthandizani kuti mudziwe zambili zokhudza Yesu, komanso mmene mungakhalile ndi umoyo wacimwemwe palipano mwa kutsatila malangizo ake. Fufuzani pa jw.org kuti mudziwe zambili, kapena pemphani kuti munthu wina aziphunzila nanu Baibo kwaulele.

Mungakondenso Izi

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBO

Coonadi Conena za Yesu

Pezani mayankho ocokela m’Baibo pa mafunso amene muli nao okhudza Yesu.

ZIPHUNZITSO ZOFUNIKA ZA M'BAIBO

N’cifukwa Ciani Yesu Anafa?

Baibo imaonetsa kuti imfa ya Yesu ni yofunika kwambili. Kodi imfa yake inali na colinga canji?