NSANJA YA MLONDA Na. 1 2016 | N’zotheka Kumvetsetsa Baibulo
Kodi munadzifunsapo kuti, ‘N’cifukwa ciani Baibulo ndi lovuta kumvetsetsa?’
NKHANI YA PACIKUTO
N’cifukwa Ciani Tifunika Kumvetsetsa Baibulo?
Anthu ambili amalemekeza kwambili buku lopatulika limeneli koma sadziwa mmene lingawathandizile.
NKHANI YA PACIKUTO
Buku Losavuta Kumvetsetsa
Mfundo zinai zimene zionetsa kuti anthu amitundu yonse akhoza kumvetsetsa Baibulo.
NKHANI YA PACIKUTO
Pemphani Thandizo Kuti Mumvetsetse Baibulo
Ngati n’zotheka kumvetsetsa Baibulo, n’cifukwa ciani mufunika thandizo kuti mulimvetsetse?
Cinyengo, Kodi Cidzatha?
Kodi anthu onyenga akuthandizani kusiya zandale, cipembedzo, kapena zamalonda?
Kodi Mudziŵa
Kodi Ayuda amene anapezeka pa Pentekosite mu 33 C.E. anacokeladi “mu mtundu uliwonse mwa mitundu ya pansi pa thambo”? Kodi anthu masauzande ambili amene anali kubwela ku Yerusalemu kudzacita zikondwelelo zaciyuda anali kugona kuti?
TENGELANI CIKHULUPILILO CAWO
“Mwana Wanga Wokondedwa ndi Wokhulupilika mwa Ambuye”
N’ciani cinathandiza Timoteyo wacinyamata amene anali wamanyazi kuti akhale woyang’anila wabwino wacikristu?
Kuyankha Mafunso a m’Baibulo
Ngati akufa adzaukitsidwa, kodi adzakhala kuti?
Mungakondenso Izi
ZOKHUDZA IFE MBONI
Pemphani kuti wa Mboni adzakucezeleni
Kambilanani nkhani ya m’Baibo na Mboni za Yehova, kapena laŵani maphunzilo a Baibo amene timapeleka.

