M’bale wacinyamata akuphunzitsidwa mu mpingo

UMOYO NA UTUMIKI WATHU–KABUKU KA MISONKHANO July 2019

Makambilano Acitsanzo

Makambilano otsatizana-tsatizana okamba za cimene cimacititsa mavuto na mmene adzathela.

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Vulani Umunthu Wakale, Muvale Watsopano

Pambuyo pa ubatizo tifunika kupitilizabe kuvula umunthu wakale na kuvala watsopano.

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Pitilizani Kutonthozana ndi Kulimbikitsana”

Aliyense wa ife angakwanitse kulimbikitsa ena. Motani?

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Wosamvela Malamulo Aonekela

Cinsinsi ca “wosamvela malamulo” cokambidwa pa 2 Atesalonika 2 civumbulidwa.

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Kalamilani Nchito Yabwino

Abale obatizika, kuphatikizapo amene akali acicepele, afunika kukalamila. Motani?

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Mungaphunzile Ciani kwa Iwo?

Ngati ndinu mtumiki wothandiza kapena mkulu watsopano, kodi mungaonetse bwanji kuti mumalemekeza aciyambakale? Nanga mungacite ciani kuti muphunzile kwa iwo?

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Kudzipeleka kwa Mulungu Kapena ku Cuma

N’cifukwa ciani tingakhale acimwemwe kwambili ngati tadzipeleka kwa Mulungu m’malo mofuna-funa cuma?

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kudzipeleka Kwa Mulungu na Kucita Maseŵela Olimbitsa Thupi

Ni mfundu za m’Baibo ziti zimene zingathandize Akhristu kuona maseŵela olimbitsa thupi moyenelela?