GALAMUKA! Na. 1 2025 | Mungatani Zinthu Zikakwela Mtengo?

Kodi muli ndi nkhawa cifukwa ca kukwela mtengo kwa zinthu zofunika pa umoyo? Kodi mumagwila nchito kwa maola ambili kuti mupeze zofunikila? Kodi mumakhala ndi nthawi yocepa yoceza ndi a m’banja lanu? Ngati n’conco, nkhani za m’magazini ino ya Galamuka! zidzakuthandizani. Nkhanizi zili ndi malangizo amene angakuthandizeni kukhalabe acimwemwe komanso kucepetsa nkhawa yanu. Nkhani yothela ikamba za ciyembekezo cabwino kwambili cokhudza tsogolo lathu, ndipo ifotokoza mmene ciyembekezo cimeneci cingakuthandizileni palipano.

 

Kungobvomeleza Mmene Zinthu Zilili

Kubvomeleza mmene zinthu zilili kungatithandize kucepetsako nkhawa.

Muzisewenzetsa Ndalama Zanu Mwanzelu

Onani zinthu zisanu zimene mungacite kuti muzisewenzetsa ndalama zanu mwanzelu.

Muzikhala Okhutila

Phunzilani mmene mungakhalilebe acimwemwe ngakhale pamene muli ndi zocepa.

Khalani Owolowa Manja

Kodi kupatsa ena mowolowa manja kungakuthandizeni bwanji kupilila mavuto azacuma?

Khalani ndi Ciyembekezo

Baibo imapeleka ciyembekezo cotsimikizika ca tsogolo labwino, ndipo ciyembekezoco cingakuthandizeni palipano.

Dziwani Zambili

Baibo ikuthandiza anthu ambili kupilila bvuto la kudula kwa zinthu. Inunso ingakuthandizeni.