CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | GENESIS 40-41
Yehova Anapulumutsa Yosefe
41:9-13, 16, 29-32, 38-40
Yosefe anavutika monga kapolo komanso mkaidi kwa zaka pafupi-fupi 13, Yehova asanam’pulumutse pa mavuto ake. M’malo mokhumudwa, Yosefe anaphunzila zinthu zabwino zambili pa zimene zinam’citikila. (Sal. 105:17-19) Iye anadziŵa kuti Yehova sanamusiye ngakhale pang’ono. Ndipo anacita zonse zotheka malinga na mmene zinthu zinalili mu umoyo wake. Motani?
-
Iye anali kugwila nchito molimbika komanso anali wodalilika, mwa ici Yehova anadalitsa khama lake.—Gen. 39:21, 22
-
Anali kucita zinthu mokomela mtima anthu ena, m’malo mokhala na maganizo ofuna kubwezela amene anam’citila zoipa.—Gen. 40:5-7
Kodi citsanzo ca Yosefe cinganithandize bwanji kupilila mavuto anga?
Ningayesetse bwanji kumacitabe bwino m’mikhalidwe iliyonse mpaka pamene Yehova adzanipulumutse pa Aramagedo?

