Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Ninganyamuke

Ninganyamuke

Daunilodi:

  1. 1. Mtima wanga wavutika

    N’thandizeni.

    Nidziŵa zimene ninalakwa

    Nili na cisoni, conde nithandizeni,

    Kuti nibwelele kwa inuyo.

    (KOLASI)

    Zonse munaniphunzitsa nikumbukila

    Coonadi ca mu Mawu Anu;

    Kuti nikakhumudwa kapena kugwa

    Ninganyamuke.

  2. 2.Nidzabwelela kwa ‘bale

    okonda Yehova.

    Amasamaladi za ine.

    Nipempha Yehova, kuti ine nibwelele

    Panjila ya kumoyo wosatha.

    (BILIJI)

    Zonse niona, zinikumbutsa coonadi canu:

    Mapeto afika.

    (KOLASI)

    Nipempha muniyankhe

    Pemphelo langa

    Nifunitsitsa thandizo lanu.

    Inu mudziŵa kuti nimalakwa

    Nidzanyamuka.

    (BILIJI)

    M’lungu amanimvetsetsa

    Iye adzanithandiza

    Amaona zimene zili mumtima wanga

    Anifunila zabwino.

    (KOLASI)

    Lelo nipita kusonkhana

    Nikatonthozedwe.

    Nibwelela kwa Yehova.

    Ngakhale nikhumudwe

    Ngakhale nigwe

    Nidzanyamuka

    Ninganyamuke.